Nkhani

Chimanga cha k1bn chaola ku admarc

Komiti ya za malimidwe ku Nyumba ya Malamulo yatulukira kuti chimanga cha ndalama zokwana K1 billion chaola mu nkhokwe za Admarc.

Koma mkulu wa Admarc, Margaret Roka Mauwa, wakana kuthirirapo ndemanga pa lipotilo kaamba koti sadalilandire.

Admarc iyenera kupeza njira zosamalira chimanga chake

Popereka lipoti lake ku nyumbayo, komitiyo yati ngakhale izi zili choncho,  Admarc ikugulitsabe kwa anthu chimangacho.

“Komiti yathu yapeza kuti chimanga cha ndalama zosachepera K1 biliyoni ndipo n’cholemera matani 7 000 n’choola mu nkhokwe za Admarc.

“Chokhumudwitsa n’choti Admarc ikupitiiriza kugulitsa chimangacho kwa anthu,” likutero lipotilo.

Lipotilo lidawerengedwa ndi Sameer Suleman ndi Werani Chilenga.

Komitiyo idatulukira izi pomwe imakumana ndi akuluakulu ochokera m’mabungwe omwe ali pansi pa unduna wa zamalimidwe pokonzekera kukambirana bajeti ya 2019/20.

Koma Mauwa adati n’kovuta kuthirirapo ndemanga pa nkhaniyo kaamba koti sadalandire lipotilo.

“Pakhala povuta kuti ndiyankhe kaamba koti lipotilo sindinalione, komanso kudalibe komwe amaliwerenga.

“Pakatipa zambiri zakhala zikundidutsa kaamba koti ndinali m’chipatala,” adatero mkuluyu.

Katswiri wa zaulimi, Tamani Nkhono Mvula, adati n’zokhumudwitsa kuti Admarc ikugulitsa chimanga choonongeka kwa anthu.

Mkuluyu  adati zaka zowerengeka zapitazo Admarc idakumana  ndi vuto ngati lomwelo ndipo anthu amayembekezera kuti adatolapo phunziro.

“Kodi n’zoona tizimva kuti chimanga chaonongeka ku Admarc? Kodi chifukwa chiyani sititolapo phunzira pa chimanga chaboma chomwe chidaonongeka posachedwapa n’kupeza njira zothandiza kuthana ndi vutoli?

“Kodi zimatheka bwanji chimanga kumaolera mu nkhokwe za Admarc anthu akumabwerera m’misika yake kaamba kosowa chimanga? Ndimamva chisoni kwambiri ndi dziko lathu,” adatero Nkhono.

Katswiriyu adati Admarc siikuyenera kugulitsa chimanga choonongeka kaamba koti n’choopsa pa moyo wa munthu.

Kafukufuku akuonetsa kuti mbewu zoola zimakhala ndi chuku chomwe chimayambitsa matenda osiyanasiyana kuphatikizirapo a khansa.

Mu 2013 chimanga cholemera matani 60 000 chidaoleranso mu nkhokwe za Admarc ngakhale pa nthawiyo anthu ambiri amagona m’misika yake kufuna kuchigula.

Aphungu a komitiyo apempha boma kuti lipereke ndalama ku Admarc zoti igulire matani 96 000 a chimanga kuti anthu asafe ndi njala m’dziko muno.

Malingana ndi lipoti la Mvac, anthu oposa 3.3 miliyoni akumana ndi vuto la chakudya chaka chino. Mwa anthuwa, 1.8 miliyoni ndi ochokera m’chigawa cha kummwera.

Alimi ambiri m’chigawochi sadakolole mokwanira kaamba ka ng’amba, komanso vuto la madzi osefukira womwe adasesa mbewu zawo.

Komitiyo yapezanso kuti Admarc ikulipira anthu pafupifupi 900 omwe sagwira ntchito ku bungwelo moti yapempha boma kuphwasula bungwelo n’kuipanganso pofuna kuthana ndi vutolo.

Komitiyi yapemphanso boma kuti liwonjezere anthu omwe akuyenera kupindula ndi zipangizo zotsika mtengo kuchokera pa 900 000 n’kufika pa 1 miliyoni.

Padakali pano ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengo adaipatsa K35.5 biliyoni.

Related Articles

Back to top button