Nkhani

Mutharika afika mawa

Listen to this article

Mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, afika m’dziko muno mawa kuchokera ku America komwe adakakhala nawo pa msonkhano wa bungwe la maiko onse la United Nations.

Katswiri wa za ndale, George Phiri, wati Mutharika wachita bwino kubwera kuti adzakonze mavuto omwe agwa m’dziko muno ali kunja.

Wadukiza ulendo wake: Mutharika

Phiri amanena za zipolowe zomwe zidachitika pakati pa ochita zionetsero ndi anyamata omwe adavala makaka a chipani cha Democratic Progressive Party (DPP).

Anyamatawo adatema anthu ndi akuluakulu a bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) omwe amachita zionetsero zofuna kukakamiza wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), Jane Ansah, kuti atule pansi udindo wake kaamba koti sadayendetse bwino zisankho za pa Meyi 21.

Pofuna kukhazikitsa bata, apolisi adaponyera anthu utsi wokhetsa misonzi ndipo wina udakagwera ku chipatala cha Gulupu komwe udadzetsa mpanipani pakati pa odwala ndi madotolo mpaka mayi wina woyembekezera adakomoka nawo.

Ena mwa anthu omwe adakhapidwa ndi mmodzi mwa akuluakulu a HRDC, Billy Mayaya.

Adamson Muula, m’modzi mwa madokotala komanso aphunzitsi a pa sukulu ya madotolo ya College of Medicine (CoM), alembera  kalata mkulu wa apolisi Duncan Mwapasa yosonyeza kukhumudwa ndi mchitidwe woponyera utsi ku chipatala.

Mkulu wa bungwe la Malawi Health Equity Network, George Jobe, naye adati ndi wokhumudwa ndi mpungwepungwe womwe apolisi adadzetsa ku Gulupu.

“Chokhumudwitsa n’choti apolisi sakusankha malo woponya utsi wokhetsa misonzi moti wina udagwera ku Gulupu mpaka mayi woyembekezera kukomoka nawo,” adatero Jobe.

Ichi n’chifukwa chake Phiri akuyamikira Mutharika kaamba kodukiza ulendo wake kuti azathana ndi mavutowa.

Kalata yolengeza kubwera kwa Mutharika yachokera ku nyumba ya boma ndipo ikuti mtsogoleriyu atera pa bwalo la ndege la Kamuzi Internatioal Airport (KIA) Mawa.

Related Articles

Back to top button