Nkhani

Chipulula mu DPP

Listen to this article

Masankho a ndime ya chipulula (mapulaimale) ayamba ndi moto m’chipani cha Democratic Progressive Party (DPP).

Lolemba lapitali yemwe adali mkulu wa bungwe la fodya la Tobacco Control Commission (TCC) komanso adakhalako woyang’anira nyumba yachifumu ya mtsogoleri wa dziko lino Bruce Munthali, adagwa

Adazitaya: Munthali

chagada kumpoto m’boma la Mzimba. Iyeyu amapikisanana ndi Rosemary Mkandawire yemwe adali mkulu wa Toyota Malawi.

Pomwe Mkandawire adapeza mavoti 407 pamalo wovotera oyamba a Elunyeni, Munthali adasiyidwa pa mphepo  ndi voti yake yokha basi. Apa mpomwe adangozitaya, poona kuti ngakhale apitirire kumalo ena 7 otsalawo saphula kanthu.

Munthali adati ngakhale padali zovuta zina zomwe sadafune kuzitchula iye wasankha kuvomereza kulephera.

“Ndalephea, ndipo ndavomereza kuti ndagwa pamasankho a chipulula. Ndigwira ntchito ndi mnzanga amene wapambanayu popititsa patsogolo mgwirizano m’chipani chathu,” adalongosola Munthali.

Yemwe amayang’anira masankhowa Songazaudzu Sajeni adati monga woyendetsa zisankhozo, zomwe zidachitikazo zidawapatsa mphepo.

“Nafe tidamera tsemwe titaona kuti anthu onse apita pambuyo pa mayi Mkandawire n’kuwasiya a Munthali wokha,” adalongosola Sajeni.

Zisankhozi zidapitilira opanda Munthali ku madera monga Kamwe, Engucwini, Ezondweni, Enukweni, Luzi ndi Kacheche.

Nako kumpoto m’boma la Karonga, Mungasulwa Mwambande adadutsa wopanda wopikisana naye. Iyeyu amayenera kupikisana ndi yemwe ndi phungu pakadalipano Vincent Ghambi koma adalowa gulu la UTM.

Ndipo Lachitatu, mapulaimale adaliko ku Nkhata Bay pomwe ofuna uphungu atatu Vuwa Kaunda kudera la pakati, Happy Chirwa m’dera la kummwera komanso Etta Banda kummwera cha kummawa adadutsa popanda opikisana nawo. M’dera la kumpoto cha kumadzulo Julius Chione adagonjetsa David Kaweche, yemwe adakhalapo phungu wa deralo.

M’chigawo cha kummwera, zisankho za ndime ya chipululazi ziyamba pa 15 ndi boma la Nsanje.

Akadaulo ena koma ati njira yoimika anthu kumbuyo kwa yemwe akumufuna siyabwino chifukwa ena amaimira mantha.

Katswiri pankhani za ndale, Nandini Patel adati kavotedweka n’kopangitsa ena kuvotera munthu yemwe sakumufuna poopa kunenedwa komanso posangalatsa abale, anansi ndi atsogoleri a zipani.

Pomwe Humphrey Mvula adati andale ambiriwa amakopa ovota ndi ndalama.

“Choncho akaluza, amawakwiyira anthu aja adawadyera aja powakhumudwitsa. Kunena chilungamo, n’zowawa kuona munthu alibe aliyense pambuyo pake polingalira nyengo yaitali yomwe imatenga kupanga kampeni,” adalongosola motero.

Related Articles

Back to top button