Nkhani

Chipwirikiti ku Malawi

Kuphwanya ndi kusalemekeza malamulo kwayala nthenje m’dziko muno. Anthu akungopha ngati akupha nkhuku, kugwiririra, kuononga ngakhalenso kuyatsa katundu.

Sabata yatha, anthu awiri adakhapidwa ndi kuphedwa ku Neno powaganizira kuti ndi mfiti ndipo sipanathe nthawi pomwe anthu enanso adaphedwa kwa Chitukula ku Lilongwe pamkangano wa malo.

Naye adagendewa: Mayaya

Izi zili apo, Akhristu ndi Asilamu adalikitana ku Balaka pomwe sukulu ya mpingo wa Anglican ya M’manga idaletsa atsikana kuvala mipango yotchinga kumutu potsatira chipembedzo cha Chisilamu.

Ndipo izi zili mkamwamkamwa, msilikali wina adapha asilikali anzake awiri ku Ntcheu ndipo naye adaomberedwanso ndi apolisi a kuusilikali. Ndipo si kale pomwe nyumba 21 zidaotchedwa ku Nkhata Bay ndipo anthu 4 adaphedwa pa zipolowe.

Si kale pomwe anthu otsatira chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) adagenda ndi kuvulaza mmodzi mwa omenyera ufulu wa anthu Billy Mayaya pa zionetsero zimene bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) limachita pofuna kukakamiza mkulu wa bungwe la Malawi E;ectoral Commission (MEC) Jane Ansah atule pansi udindo. Ndipo wapolisi wina adaphedwa ku Nsundwe m’boma la Lilongwe pomwenso apolisi ena akuwaganizira kuti adagwirira ndi kulanga amayi ndi asungwana ena.

Nako ku Karonga, pofuna kusatsalira pa mpungwepungwe wabukawu, kudali anthu ena kuvula amayi ndi atsikana ngati avala mathalauza ndi siketi zazifupi m’bomalo.

Izi zikuchitika ngakhale lamulo loyendetsera dziko lino limati kuli ufulu wa kavalidwe. Ndipo amabungwe oteteza ufulu wa anthu  monga Foundation for Community Support Services (Focus) adzudzula mchitidwewu ndipo apempha apolisi kuti atsekere m’chitokosi wachinyamata aliyense amene akuvula amayi.

Pakadalipano mkulu wa apolisi m’bomalo Sam Nkhwazi wati sadamangeko munthu pokhudzana ndi nkhaniyi.

Malinga ndi Mfumu Malema 2 ya m’boma la Karonga, iwo adakhazikitsa malamulo woti ana a sukulu (anyamata ndi atsikana) asamapezeke kunyanja chifukwa zinthu zidafika poipa ndipo anawa amachita zolaula kunyanjako.

Iye adati atakhala pansi adakhazikitsa gulu lomakayendera kunyanjako ndi kumagwira tiana tomwe amatipeza komanso adapeza galimoto yomwe idalengezetsa Lachisanu lapitalo kuti anawa asapezeke kunyanja ndipo akangopezeka agwidwa.

“Tidachita izi chifukwa anawa adaonjeza kuthawa kusukulu n’kumabwera kunyanja kukamwa mowa ndi kugona ndi amuna. Chidatikhudza kwambiri ndi choti mwana wina wa zaka 13 adamwetsedwa mowa patsiku la anakubala ndi kugonedwa ndi anyamata ambiri. Anawa amakhala oti athawa m’sukulu,” adatero Malema.

Koma iye adakanitsitsa kuti adakhazikitsa malamulo oti amayi asamavale mathalauza ndi siketi zazifupi m’bomalo.

“Izo akupanga ndi akabaza kumsika ndipo ife sizikutikhudza,” adatero iye.

Pomwe mayi wina yemwe adaona mnzake akuvulidwa, Christobel Shaba, adati zikuchitika m’bomalo ndi zoopsa ndipo amayi akukhala ndi mantha akulu.

Polankhulapo pa chipwirikiti chomwe chikuchitikachi, mphunzitsi wa ufulu wa anthu pasukulu ya ukachenjede ya University of Livingstonia George Phiri adati zonsezi zikungosonyeza kuti utsogoleri wa dziko lino walephera.

Phiri adatinso n’zokhumudwitsa kuti mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika sakuonetsa chidwi chofuna kuthetsa mavuto m’dziko muno ndipo wangoti duuu!

“Tangoganizani, wamkulu wa apolisi adabwera poyera n’kunena kuti apolisi alibe kuthekera kopereka chitetezo m’dziko muno, kodi mtsogoleri wa dziko lino adachitapo chiyani izi zitanenedwa? Kodi mtsogoleriyu akuona zikuchitikazi? Nanga bwanji wangoti duuu! ndipo palibe chomwe akuchitapo?” adatero Phiri.

Koma nduna ya zofalitsa nkhani Mark Botomani idatsutsa kwa mtu wa galu kuti utsogoleri wa dziko lino walephera. Botomani adati ngakhale akugwirizana ndi zoti zikuchitika m’dziko muno ndipotsa mantha komanso zoziziritsa  thupi chifukwa anthu akungotengera malamulo m’manja mwawo, koma mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika akuyesetsa kukonza zinthu kuti zibwelere m’chimake.

“Ifeyo ku boma kuno tikuona kuti abweretsa chimzimu choipachi m’dziko muno  ndi a mabungwe omwe amakonza zionetsero zoti mtsogoleri wa bungwe la Malawi Electoral Commission [MEC] Jane Ansah achoke chitangochitika chisankho cha pa 21 May,” adatero Botomani. n

Related Articles

Back to top button