Chipwirikiti pachisankho
Pali chipwirikiti pachisankho cha mtsogoleri wa dziko lino, pomwe wapampando wa bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah wapempha Nyumba ya Malamulo kuti isankhe tsiku lochitira chisankhocho.
Izi zikudza pomwe mmbuyomu Nyumba ya Malamuloyo idapempha mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti avomereze chisankhocho chidzachitike pa 19 May. Koma Mutharika adakana kusainira bilo ya nyumbayo, pomwe MEC idaika 2 July ngati tsiku lochitira chisankhocho potengera ndi chigamulo cha bwalo la milandu la Constitutional Court lomwe lidati chisankho chichitike pasanathe masiku 150.
Popereka lipoti ku mbali zonse zokhudzidwa ndi chisankho la National Electoral Consultative Forum (Necof) ku Mangochi Lachitatu, Ansah adati chigamulo cha bwalo lalikulu la Supreme Court chiyenera kuganizira za miyoyo ya anthu omwe akufuna kuti adzawavotere kuti adzawatsogolere zaka zikudzazi.
“Mtsogoleri sangakhale waphindu ngati anthu omwe akutsogolera akudwala, tsono apa tikukamba za matenda owopsa a Covid-19. Tikamba nawo kuti tione momwe tingathandizirane nawo,” adatero Matemba.
Pomwe katswiri pa ndale Musatafa Hussein adati chomvetsa chisoni n’choti anthu omwe amayenera kutsogolera kupewa matendawa, ndiwo akutsogolera kuphwanya ndondomeko zowapewera.
“Nkhani ili apa ndi ya moyo kapena imfa tsono timayenera kukhala osamala kwambiri. Boma silopusa kuyika ndondomeko koma atsogoleri ndiwo akuyambitsanso kuphwanya,” adatero Hussein.
Nduna ya zaumoyo Jappie Mhango yemwenso akutsogolera komiti yapadera yoyendetsa za kapewedwe ka matendawa adati sakukondwa ndi zomwe zipani za ndale zikupanga.
“Akuganizira zawo zokha ndi cholinga chodzapambana mavoti koma akuyika miyoyo ya anthu pachiswe. Kunena zoona,” adatero Mhango.
Amalawi ena omwe alankhula ndi tamvani ati nawo sakukondwa ndi misonkhanoyo polingalira kuti iwo akulephera kupanga zitukuko chifukwa boma lidaletsa ntchito zina monga mabizinesi.
Matenda a Covid-19 adapezeka koyamba m’dziko la China kumapeto kwa chaka chatha ndipo bungwe la zaumoyo pa dziko lonse la WHO lidalengeza kuti matendawo ndi m’lili wadziko lapansi.
Anthu zikwizikwi amwalira m’mayiko ambiri padziko lonse ndipo M’malawi muno anthu 56 adapezeka ndi matendawo pomwe atatu ndiwo adamwalira.
Dziko la Malawi lidakhazikitsa ndondomeko zopewera matendawo kuphatikizapo kuletsa misonkhano ya anthu oposa 100, kusamba m’manja mwakathithi, kusintha makhalidwe a m’magalimoto, kutseka sukulu ndi kupeleka tchuthi kwa ogwira ntchito zina m’boma.
Padakalipano MEC ikufuna kugula zipangizo zodzitetezera pamene akukonzekera chisankhocho.