Chisankho chizichitika mu September
Aphungu a Nyumba ya Malamulo Lachitatu adavomereza bilo yosintha tsiku la chisankho kuchoka sabata yachitatu ya mwezi wa May kufika sabata yachitatu ya September.
Tsiku la tsopanoli liyamba kugwira ntchito pachisankho cha 2025. Kusinthako kwachitika kaamba koti September kumakhala kotentha poyerekeza ndi May pomwe kuzizira ndi mawawa kumasokoneza kuvota.
Kuyambira 1994 pomwe chisankho cha zipani zambiri chidachitika, malamulo akhala akunena kuti chisankho chizichitika Lachiwiri la sabata yachitatu ya May.
Kusinthako kwadzanso pamene aphunguwo adakhazikitsa kuti phungu amene wapambana azikhala amene wapeza mavoti ochuluka kuposa anzake, osati kupeza mavoti oposa 50 mwa 100 alionse monga zilili ndi wopambana pa upulezidenti.
Kusinthako kudadza pomwe wapampando wa bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) Chifundo Kachale adati opambana pa zisankho zapadera za aphungu zimene zichitike posachedwa adzapeze mavoti oposa 50 mwa 100 alionse.
Malinga ndi nduna ya za malamulo Titus Mvalo, yemwe adabweretsa mabiluwo, adati kutsata ndondomeko yoti phungu wopambana azipeza mavoti oposa 50 pa 100 iliyonse ndiye kuti MEC izichititsa zisankho zambiri zachibwereza zomwe zingachititse dziko lino kuononga ndalama zambiri.
“Bwalo la milandu limagamula nkhani ya mtsogoleri wa dziko osati aphungu. Likadakhala kuti bwalolo limafunanso kuti aphungu ndi makhansala azipeza mavoti oposa 50 mwa 100 alionse, likadaneneratu mwa mvemvemve,” adatero Mvalo.
Mneneri wa chipani cha DPP pa za malamulo Bright Msaka adati bungwelo lidaphophonya.
“Aphungu sakhala ndi mphamvu ngati zomwe zili ndi mtsogoleri wa dziko lino. Pulezidenti amalamulira dziko lonse, choncho ayenera kupambana ndi mavoti a anthu ochuluka kwambiri,” adatero Msaka.
Kadaulo pa ndale George Phiri adati aphunguwo adapanga chiganizo chakupsa povomera kusintha lamulolo.
“Vuto lomwe lilipo ndi loti aphungu ndi makhansala ndi ambiri komanso pachisankho amasiyana ndi mavoti ochepa kwambiri kotero kuti kukhoza kukhala zisankho zachibwereza m’madera a aphungu ndi makhansala onse.
“Potengera momwe thumba lathu lilili, izi n’zosatheka moti mapeto ake mutha kumaona kuti chisankho chikachitika, pakutenga nthawi yaitali tikudikira thandizo la zachuma cha chisankho china ndipo panthawiyo madera ambiri atha kumakhala opanda phungu kapena khansala,” adatero Phiri.
Ndipo biloyo ikutambasulanso kuti pazidutsa masiku a pakati pa 7 ndi 30 mtsogoleri wa dziko asanamulumbiritse komanso aphungu amene alipo panowa akhala zaka 6 mmalo mwa 5 kuti chisankho cha patatu chidzatheke mu 2025.
Padakalipano, aphunguwo amayembekezeka kukwangula msonkhano wawo dzulo. Iwo akhala akukambirana kuchokera pa 5 October ndipo pambali povomereza bajeti ya momwe boma ligwiritsire ntchito ndalama zake, iwo adavomerezanso mabilu angapo.
Iwo adavomereza bilu yoti anthu amene amalandira K100 000 asamakhome msonkho wa ogwira ntchito ndipo boma lizidula K20 pa K100 iliyonse yomwe munthu wapata pochita juga.
Izi zikutanthauza kuti ngati munthu wapata K100 pa juga monga ya Premier Bet, yake izikhala K80 ndipo K20 izipita kuboma.
Izi zadandaulitsa mneneri wa chipani cha DPP pa zachuma Joseph Mwanamvekha yemwe adati: “Msonkho pa juga n’kupha achinyamata chifukwa akudalira jugayo n’kusowa kwa ntchito masiku ano.” n