Chitetezo chaphwasuka
Chitetezo chaphwasuka. Anthu akuberedwa, kumenyedwa ndi kuchitidwa zachipongwe zambiri. Akaitanitsa apolisi akuti akumatenga nthawi kuti abwera ndipo nthawi zina sabwera. Izi zikukhumudwitsa anthu ndi mafumu.
Koma wachiwiri kwa mneneri wa polisi m’dziko muno, Thomeck Nyaude, watsutsa nkhaniyi. Iye wati apolisi akalandira uthenga sanyozera, koma amathamangira komwe kwavutako.
T/A Nyambi ya m’boma la Machinga yati chidodo cha apolisi ndicho chikuchititsa kuti anthu azilanga okha akagwira munthu yemwe akumuganizira kuti ndi wamtopola.
Nyambi amathirira ndemanga pa nkhani yoti anthu okwiya adazunza atolankhani a BBC ku Karonga powaganizira kuti ndi anamapopa.
Anthu adamenya atolankhaniwo, kuwalanda zipangizo zawo ndi kuswa galimoto yawo. Izi zidachitika kwa maola oposa 7, koma apolisi sadatulukire.
Nako ku Machinga akuba adathira machaka mfumu Kawinga n’kuibera ndalama zoposa K1 miliyoni, koma akuti apolisi sadalanditse mfumuyo ngakhale adadziwitsidwa.
Koma Nyaude watsutsa ndipo wati anthu ambiri sadziwitsa apolisi zikawathina. “Ndife anthu sitigwiritsira ntchito mphamvu zamatsenga. Timadalira kuuzidwa ndipo ngati sadatiuze ndiye tigwira ntchito bwanji?”
Iye wati nkhani ya atolankhani a BBC idakhota chifukwa atolankhaniwo sadawadziwitse kuti akutsikira m’midzi ya Karonga.
“Adangopita kuderako osatidziwitsa. Amangoganiza kuti zinthu zili bwino, ndiye masiku ake si anowa.”
Atolankhaniwo, Dariud Gregory Barzagan, Ahmed Hussein Divela ndi Prince Anus Asamoah adathambitsidwa ndi anthu olusa a m’dera la Malema pamene amalemba nkhani zokhudzana ndi matsenga.
Iwo adatsogozedwa ndi mtolankhani wa m’dziko muno Henry Mhango komabe izi sizidasinthe kanthu pamene anthu am’mudziwo adaloza zala atolankhaniwo kuti ndi anamapopa.
“Nkhani zomwe amalembazonso zidali zosavuta kuti anthu alumikize ndi nkhani zopopa magazi. Amayenera atidziwitse kuti tikhale tikuponyako maso,” adatero Nyaude.
Pa nkhani ya kuvulazidwa kwa mfumu Kawinga yomwe idalephera kuthandizidwa ndi apolisi, Nyaude wati palibe amene amayembekezera kuti izi zichitika.
“Palibe amayembekezera kuti izi zichitika, kudalinso kovuta kuti tidziwe kuti tikalanditse mfumu yathu. Tidakauzidwa, tidakathandiza, tiyeni tidalirane,” adatero Nyaude.
Koma mkulu wa bungwe loona za ufulu wachibadwidwe wa anthu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), Timothy Mtambo, wati vuto ndi apolisi komanso boma amene akulephera kuteteza anthu.
“Takhalapo ndi nkhani zopopa magazi komanso kupha anthu achialubino zomwe anthu samakhutira ndi momwe apolisi amagwirira ntchito. N’chifukwa chake anthu akumalanga okha zotere zikachitika,” adatero Mtambo.
Iye adati mavutowa akudza chifukwa apolisi akulephera kugwira bwino ntchito ndi anthu kuti azithandizira kubweretsa chitetezo.
“Tili ndi nkhani zambiri zomwe mutu wake sudziwika ndipo chomwe timamva ndi kuti akufufuza. Izitu ndi zomwe anthu alibenso chikhulupiriro ndi polisi yathu,” adatero.
Padakali pano, mfumu Kawinga yatulutsidwa m’chipatala cha Mwaiwathu ku Blantyre komwe yakhalako sabata zitatu.
Mfumuyi idaomberedwa pamwendo kawiri, kukhapidwa ndi chikwanje paphewa, pamkono komanso kumenyedwa ndi chitsulo pamwendo.
Polankhula ndi Tamvani sabata yatha, Kawinga adati akubawo adaomberanso mlonda wake komanso kuvulaza mwana wake.
“Izi zimachitika atandibera K1 miliyoni komanso 200 euros. Adaphwanyira galimoto ziwiri,” adatero.