Nkhani

Zikhulupiriro zikufalitsa kolera—unduna

Unduna wa zaumoyo wati zikhulupiriro ndizo zikuchititsa kuti chiwerengero odwala kolera chizikwera.

Koma bungwe la United Nations Children’s Fund (Unicef) lati kafukufuku wawo waonetsa kuti kusowa kwa madzi aukhondo ndiko kukukolezera matendawa m’dziko muno.

Malingana ndi undunawo, chiwerengero cha anthu omwalira ndi kolera chafika pa 10 pamene odwala matendawa m’maboma 13 a m’dziko muno chapitirira 546.

Mneneri wa undunawu, Joshua Malango, wati chiwerengero cha odwala kolera sichikutsika kaamba koti anthu ambiri sakuthamangira ku chipatala akaona zizindikiro za matendawa.

“Si kuti anthu sadamve uthenga, koma ambiri akumapita ku chipatala mochedwa. Mwachitsanzo, wodwala wina wamwalira ku Salima kaamba koti adapita naye ku chipatala patatha maola 7 atayamba kudwala kolera,” watero Malango.

Mkuluyu wati anthu ena akumamwa mankhwala azitsamba akadwala kolera poganiza kuti alozedwa.

“Zikhulupiriro zikukolezeranso kolera m’dziko muno. Titafufuza tapeze kuti anthu 7 amwalira kaamba ka zikhulupiriro mmalo mothamangira ku chipatala amathamangira kwa amsing’anga,” watero Malango.

Anthu anayi amwalira ndi kolera ku Karonga pamene ku Lilongwe anthu asanu ndiwo amwalira ndi matendawa.

Mwa anthu 546 odwala kolera, 277 ndi ochokera m’boma la Karonga, 164  Lilongwe, 44 Salima, 20 Nkhata Bay, 9 Rumphi, 5 Dowa ndi 4 Mulanje. Ku Kasungu, Dedza, Blantyre ndi Chikwawa kwamwalira munthu mmodzimodzi.

Mkulu wa bungwe la Unicef, Johannes Wedeing, wati matenda a kolera avuta kaamba kosowa madzi aukhondo m’madera osiyanasiyana a m’dziko muno.

“Tayeza madzi ndipo tapeza kuti zitsime zambiri makamaka za m’boma la Lilongwe ndi zokhudzidwa ndi tizilombo toyambitsa kolera,” watero Wedeing.

Mkulu woona za chitukuko ku khonsolo ya Lilongwe, Douglas Moffat, wati akukambirana ndi a Lilongwe Water Board kuti apeze njira zochepetsera vuto la madzi m’bomalo.

Mkulu wa zaukhondo ndi zachilengedwe mu khonsolo ya Blantyre, Penjani Chunda, wauza atolankhani kuti akhazikitsa ndondomeko zoti apezeretu mankhwala wothira m’madzi a kolera kaamba koti bomali lili pachiopsezo kaamba ka vuto lakusowa kwa madzi lomwe lagwa m’bomali.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button