Chomwe aimitsira mlandu wa a muluzi chidziwika lolemba
Mkulu wa bungwe loyendetsa milandu la Director of Public Prosecutions (DPP) a Masauko Chamkakala akuyembekeza kuuza Amalawi chifukwa chomwe aimitsira mlandu wa mtsogoleri wakale wa dziko lino a Bakili Muluzi pa nkhani yokhudza K1.7 biliyoni.
A Chamkakala adakana kuulula ati auze kaye komiti yaku Nyumba ya Malamulo.
“Sindingayambe kunena zifukwa zomwe tagwiritsa ntchito pokhapokha nditakumana kaye ndi komiti yoona za malamulo ku Nyumba ya Malamulo. Ndikapereka lipoti langa ku komitiyo monga mwa malamulo,” iwo adatero.
Mkulu wa bungwe la maloya m’dziko muno a Patrick Mpaka adati a Chamkakala ayenera kuuza Amalawi zifukwa zomwe atsekera mulandu wa a Muluzi pasadafike pa 5 Juni 2023 potengera gawo 99(3) la malamulo a dziko lino.
A Muluzi adali mtsogoleri wa dziko ino kuyambira mchaka cha 1994 mpaka 2004.
Iwo adamangidwa mchaka cha 2006 ndipo mlandu wao wakhala ukuyenda pansi pa atsogoleri anayi a dziko lino: a Bingu Wa Mutharika, a Joyce Banda, a Peter Mutharika ndipo pano a Lazarus Chakwera.
Ngakhale nkhani ya kutsekedwa kwa milandu ya a Muluzi idakondweretsa anthu owakonda, akadaulo pa zamalamulo ati izi zikusonyezeratu kuti dziko la Malawi likadali kumbuyo pa nkhani yothana ndi katangale.
A Dawood Chirwa omwe ndi kadaulo pa zamalamulo ndipo amaphunzita m’dziko la South Africa adati kutsekedwa kwa mulanduwo kwaonetsa poyera nkhama za bungwe lolimbana ndi katangale la Anti-Corruption Bureau (ACB).
“Apapa ACB yavulidwa. Yaonekera poyera kuti ilibe mano ndiposo zaonetseratu kuti milandu ya katangale yokhudza akuluakulu a ndale siingayende m’dziko la Malawi,” iwo adatero.
Koma iwo adati n’zosadabwitsa kuti mulanduwo watsekedwa chifukwa akuluakulu akale a ACB adanenapo kuti mlandu wa a Muluzi udakhudza ndale.
Katswiri wina pa malamulo a Justin Dzonzi adati Amalawi amayembekezera kuona mapeto a mulanduwo.
“Sitingapake khothi vutoli koma ACB. [Zikuoneka kuu] Bungwe limeneli lidalibiletu umboni wooneka pa mulandu umenewu,” iwo adatero.
M’modzi mwa maloya a a Muluzi a Tamando Chokotho adati mulanduwo udaoneka pa mayambiliro kuti udalibe umboni okwanira ndipo sungapitilire.
“Yemwe adali amafufuza mlanduwo a Victor Banda adauza khoti kudakakhala kuti adafufuza mofatsa mlanduwo, sakadamanga a Muluzi. Komanso omwe adakhalako akuluakulu a ACB a Leyneck Matemba ndi a Lucas Kondowe adanenanso udali wovuta kuumaliza,” iwo adatero.
Koma loya wa ACB a Clement Mwala adati bungwelo lidalibe mphamvu zopitiriza mulanduwo chifukwa a Chamkakala adali ndi mphamvu zouimitsa.
M’mwezi wa Januware 2001, bungwe la atsogoleri a mipingo la Public Affairs Committee (PAC) lidapempha boma kuti litseke mlandu wa a Muluzi chifukwa umangoononga ndalama zaboma.
A Muluzi amaganiziridwa kuti adazembetsa K1.7 biliyoni yomwe idabwera ngati thandizo kuchokera ku maiko a Taiwan, Morocco ndi Libya. Koma a iwo amakana kuti ndalama zobwera ngati thandizo ku dziko sizidzera ku thumba la munthu ngati momwe ndalamazo zidadzera ku banki yawo.