Nkhani

Covid-19 ikufala ngati moto

Listen to this article

Komiti yoongolera zolimbana ndi mliri wa Covid-19 m’dziko muno yachenjeza kuti kachirombo koyambitsa matendawa kakufala ngati moto wolusa zomwe zachititsa kuti komitiyo ikhazikitse malamulo ena omwe ayambe kugwira ntchito Lolemba.

Nduna ya zaumoyo a Khumbize Kandodo Chiponda, omwe ndi mmodzi mwa apampando a komitiyo adalengeza malamulo atsopanowo Lachinayi pamsonkhano wa atolankhani ku Lilongwe.

Anthu pamzere kufuna kubayitsa katemera wa Covid-19

Iwo adalengezanso kuti Lachitatu lokha anthu 318 adapezeka ndi kachirombo ka corona, pomwe Lachiwiri adapezeka anthu 235 kufikitsa anthu onse omwe ali ndi kachiromboka pa 1 391 kuchoka pa anthu atatu m’mbuyomo pomwe boma linkakhwefulako malamulo opewera matenda.

A Chiponda amalengeza zomwe komiti yawo idagwirizana itakumana Lachitatu pomwe adapeza kuti dziko la Malawi lachoka pamzere woyamba ndipo lafika pamzere wachiwiri.

“Kuti mumvetsetse, tikamanena za mizere tikunena za kukula kwa vuto m’dziko. Mzere woyamba ndiye kuti zinthu ziliko bwino pomwe mzere wachisanu ndiye kuti zafika pa kayakaya, ndiye ife tafika pamzere wachiwiri tsopano,” adatero a Chiponda.

Izi zikutsimikiza zomwe madotolo ndi akadaulo pa zaumoyo adanena Lolemba pamsonkhano wa atolankhani kuti matendawa avuta kwambiri nyengo ya zisangalaloyi chifukwa anthu ambiri adanyozera kubayitsa katemera.

Pulezidenti wa madotolo m’dziko muno a Victor Mithi adati padakalipano m’zipatala maka malo osamalirako odwala Covid-19 kukudutsa mphepo koma akuyembekezera ntchito yobetsa nayo tulo zisangalalo zikafika.

“Panopa zikuoneka zopepuka koma tikamayandikira Khrisimasi mpaka mwezi wa January kukhala ntchito moti ogwira ntchito zachipatala adzakhala opanikizika, kusowa popumira,” adatero a Mithi.

Pomwe mkulu woona za umoyo m’madera a Ben Chilima adati matendawa afala kwambiri nyengo ya zisangalalo chifukwa chazochitika nthawiyi komanso polingalira kuti anthu ambiri sadabayitse katemera.

“Taonera m’maiko aanzathu komwe corona yatsopano yotchedwa Omicron yavuta, anthu ambiri omwe akumavutika zedi mwina kufa kumene ikawagwira ndi omwe sadalandire katemera ndiye kuno kwathu zikuoneka kuti ambiri sadabayitse,” adatero a Chilima.

Malingana ndi a Chiponda, katemera wokwana 1 587 487 ndiye adaperekedwa kwa anthu mmalo mwa anthu 11 miliyoni omwe boma lidakonza zoti libaye.

A Chiponda adati katemerayo akadalipo wambiri koma anthu akadakhulupilirabe zabodza zokhudza katemera wa corona yemwe munthu akabayitsa amatetezeka kuti asadwale mwa kayakaya akagwidwa ndi mliriwo.

Ngakhale talowa m’nyengo yazisangalalo, malamulo atsopano omwe ayambe kugwira ntchito Lolemba akuti malo omwera mowa azitsekedwa 10 koloko usiku komanso ngati anthu akukumana m’nyumba, asapitirire anthu 10.

Izi zikutanthauza kuti anthu omwe amakhulupirira kumwa zoledzeretsa ndi kuchezera akati akondwa ufulu wawo walandira malire.

Malamulo ena akuti mkumano wa mkati ngati kutchalitchi, kumpira, kumsonkhano ndi ku zoimbaimba anthu asamapose 100 koma pabwalo asamapose 250 komanso galimoto yonyamula anthu 10 kuyambira Lolemba izinyamula anthu 6 basi.

Kuyambira pachiyambi cha Covid-19 mu 2019, anthu 62 933 ndiwo adadwalako, anthu 59 000 adachira, anthu 2 310 adamwalira nayo ndipo anthu 1 391 ndiwo akudwala panopa.

Related Articles

Back to top button
Translate »