Nkhani

Dausi aseketsa aphungu

Zitsuzo sizimamuthera phungu wa m’dera lapakati m’boma la Mwanza a Nicholas Dausi.

A Dausi adadzuka pa mpando wawo m’Nyumba ya Malamulo ndi kukuwa kusonyeza kusangalala pamene mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera adauza aphungu kuti anthu a ku Mwanza ada-tumiza m’nyumbamo ana awo awiri—wamwamuna ndi wamkazi.

Dausi kusangalala ndi zomwe mtsogoleri wa dziko lino adalankhula m’Nyumba ya Malamulo. I STATE HOUSE

“Mwamuna ndi Dausi pamene wamkazi ndi [Joyce] Chitsulo ndipo pano ndikufuna kupereka m’ndandanda wa zitukuko zomwe boma langa lakwaniritsa m’boma la Mwanza,” adatero mtsogoleriyu.

Izi zidasangalatsa a Dausi moti adadzuka pa mpando wawo n’kukuwa chimwemwe chitadzadza mtsaya mpaka aphungu ena kugwidwa phwete.

Mwa zina, a Chakwera adati boma lapereka ngongole ya National Economic Empowerment Fund (Neef) yokwana K157.3 miliyoni kwa anthu a ku Mwanza, zipangizo zaulimi zotsika mtengo kwa alimi 63 584 mu zaka zinayi zomwe boma lawo lakhala likutumikira dziko lino.

“Neef yaperekanso ndalama zokwana K53.7 miliyoni kwa anthu abizinesi. Tagawa chimanga cha ndalama zokwana K1.4 biliyoni kwa mabanja 13 950 omwe akusowa chakudya m’bomalo.

“Tapereka magetsi kwa maanja 3 359, madzi kwa mabanja 550, tatsiriza kumanga sukulu za sekondale za Kawedza ndi Phete, zipatala za Galafa ndi Kalanga, komanso kukweza chipatala cha Thambani,” iwo adatero.

A Chakwera akuti m’miyezi iwiri ikudzayo atsiriza kumanga bwalo la masewero la Mwanza.
Malinga ndi malamulo ndi ndondomeko za Nyumba ya Malamulo, mtsogoleri wa dziko lino ndi amene amatsegulira zokambirana za nyumbayo.

Mtsogoleri wotsutsa boma ayankha zomwe a Chakwera alankhula sabata ya mawa.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button