Nkhani

Dollar yasowa

Listen to this article

Ntchito zambiri m’dziko muno zasokonekera kapena kuima kumene potsatira kusowa kwa ndalama zakunja zomwe zimagwiritsidwa ntchito poitanitsa katundu.

Umboni wafika pambalambanda tsopano ndi momwe mafuta ophikira opangidwa m’Malawi mom’muno akusowera m’sitolo zosiyanasiyana boma litangolengeza kuti mtengo wamafutawo utsike.

Malingana ndi mkulu wa mgwirizano wa makampani owenga mafuta m’dziko muno a Peter Ngoma, makampaniwo akulemphera kuwenga mafuta okwanira chifukwa akukanika kuitanitsa zipangizo kunja.

“Sikuti anthu aziona ngati tasiya kupanga mafuta chifukwa cha mitengo ayi koma kuti tikulephera kuitanitsa zipangizo kuchoka kunja chifukwa ndalama zakunja, makamaka dollar yaku America yomwe timagwiritsa ntchito yasowa,” adatero a Ngoma.

Iwo adati izi zipitirira ngati mitengo ya zipangizo zopangira mafuta ipitirire kukwera ndipo ngati ndalamayo siyiyamba kupezeka bwinobwino kuti makampani azitha kuitanitsa zipangizozo.

Vuto la ndalamayi lachititsa kuti makampani akuluakulu a maulendo a pandege a Ethiopian Airlines komanso Kenyan Airways kuimitsa ntchito zodula matikiti a ndege zawo m’dziko muno.

Mlembi wa mgwirizano wa makampani odulitsa matikiti a ndege a Eliza Chimbaya adatsimikiza kuti imodzi mwa makampaniwo ya Ethiopian Airlines yakhala ikudandaula kuti banki ya Reserve siyimalipira ndalama ku kampaniyo chifukwa chakuperewera kwa ndalama za America.

Ululu wa vutoli ukuthera pa Amalawi omwe amagula katunduyo kuti azigwiritsa ntchito chifukwa kukwera kwa mitengo yakatundu potsatira kusowa kwa dollar ndi kukwera kwa katundu padziko lonse, ndalama ya kwacha ikunka itsika.

Mkulu wa bungwe loimira anthu ogula katundu a la Consumers Association of Malawi (Cama) a John Kapito ati vutoli likhala likuyabwa Amalawi chifukwa ndalama ya dollar yasowa kwambiri.

Kadaulo wa zachuma ku sukulu yaukachenjede ya Catholic University of Malawi a Hopkins Kawaye adati Amalawi avale zilimbe chifukwa dziko lino limadalira kwambiri katundu wakunja.

“Zikungotanthauza kuti Amalawi akonzeke kupisa pamathero a matumba awo kuti azikhala bwinobwino ndipo anthu osaukitsitsa, makamaka akumudzi, akonzekere ululu waukulu,” adatero a Kawaye.

Mkulu wa bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiative (Cdedi) a Sylvester Namiwa ati ndi zomwe zikuchitikazi, boma likuyenera kusunga ndalama ya dollar yokwanira yogulira katundu wofunika kwambiri.

“Zateremu tikuyenera kuyendera kuti chofunika kwambiri n’chiyani. Pali zinthu monga mankhwala a m’zipatala, mafuta a galimoto, mafuta ophikira ndi zokhudza ulimi zoyenera kuzisungira ndalama ya dollar yokwanira,” atero a Namiwa.

Ena mwa mavuto omwe ayamba kale kuluma ndi kukwera kwa mtengo wa chimanga, womwe wafika pa K250 pa kilogalamu kapena K11 000 thumba la makilogalamu 50 kuposa mtengo wa boma wa K220 pa kilogalamu.

Mkulu wa bungwe la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) a Lekani Katandula ati vutoli likapanda kukonzedwa msanga lisokoneza ntchito zambiri zamalonda.

Koma mlembi wamkulu kunthambi ya mapulani a zachuma ndi chitukuko a Winford Masanjala ati Amalawi ayenera kudekha chifukwa mavuto a kusowa kwa ndalama zakunja siatha msanga. Iwo adati makampani monga owenga mafuta ophikira akhudzidwa kaamba ka vutoli.

“Kuti katundu wina apangidwe pamafunika ndalama zakunja. Kuti tipeze ndalama zakunja, tiyenera kugulitsa katundu wochuluka kunjako,” adatero iwo.

Related Articles

One Comment

Back to top button