Nkhani

DPP, MCP alozana zala

Zipani za MCP ndi DPP zikulozana zala pa amene adayambitsa ziwawa zimene zidachitika ku mapeto a sabata yatha ku Mponela m’boma la Dowa.

Pa zipolowezo, galimoto zina zimene zidali pa mdipiti wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP m’chigawo cha pakati a Alfred Gangata zidaotchedwa ku Mponelako pomwe amachokera ku msonkhano wan dale m’boma la Ntchisi.

Zimatere, bwenzi zikoma: A Chakwera ndi a Mutharika kugwirana chanza mmbuyomu

Polankhula kwa atolankhani ku nyumba yawo ya Page House m’boma la Mangochi mtsogoleri wa DPP a Peter Mutharika adati mlembi wamkulu wa MCP a Richard Chimwendo Banda ndiwo adakonza chiwembucho.

Popanda kupereka umboni wogwirika, iwo adati: “Mchitidwe wa ziwawa ukusonyeza kuti chipani cha MCP chikadali cha nkhanza. Ziwawazi zikungosonyeza kuti chipanichi sichivomereza ulamuliro wa demokalase. Tikudziwa kuti a Chimwendo Banda ndiwo adakonza izi.”

A Mutharika adati chipani cha MCP sichikuyenera kumasonyeza kuti zipani zina zisamachititse misonkhano m’chigawo cha pakati. “Dzikoli ndi la tonse ndiye tisamadulirane malire. Komishoni ya mtendere ikuyenera kulowererapo pa nkhaniyi,” adaonjeza motero.

Koma polankhula ndi mtolankhani wathu, a Chimwendo Banda adati a Mutharika adayenera kuunguza kaye m’chipanic chawo pa nkhani ya ziwawayi asanayambe kuloza zala ena.

“Ndikuyamika kuti a Mutharika atsatira mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera podzudzula ziwawa zoterezi koma mmalo moloza zala ena amayenera kuunguza akuluakulu a chipani chawo amene mmbuyomu adanenapo zoti otsatira chipani cha MCP ayenera kuotchedwa. Ndipo taona amayi a MCP akuthamangitsidwa mpaka kuvulidwa zovala za makaka a MCP,” adatero iwo.

Ziwawa za ku Mponela zidadza pasanathe sabata imodzi kuchokera pomwe mkulu wa apolisi Mayi Meryln Yolamu adanena kuti apolisi ali kalikiliki kuthana ndi ziwawa za ndale. Komatu pofika dzulo Lachisanu palibe amene adagwidwa pokhudzidwa ndi ziwawa za sabatayi.

“Mudziwe kuti matekitivi athu amakhala akudziwa pomwe anthu akukambirana zochita ziwawa. Sitisekerera munthu,” adatero iwo pomwe amakumana ndi akuluakulu a achinyamata m’zipani zonse 23 zimene zili m’kaundula wa zipani.

Masiku apitawa Archbishop Thomas Luke Msusa a Blantyre Archdiocese ya mpingo wa Katolika adadzudzula mchitidwe wa ziwawa umene nthawi zambiri amachita ndi achinyamata.

“Kaamba ka umphawi, andale ena amapusitsa achinyamata kuti azichita ziwawa. Uku n’kulakwa kwambiri,” adatero a Msusa.

Pogwirizana ndi a Mutharika zoti komishoni ya mtendere iyenera kuchitapo kanthu pa nkhani ya ziwawa, mtsogoleri wakale wa dziko lino Mayi Joyce Banda adati zikuoneka kuti chaka chino ziwawa zifika pena.

“Mmbuyomu anthu amangomenyana koma onani pano kukutuluka zisenga. Komishoni ili ndi ntchito yaikulu yoluzanitsa Amalawi kuti tipewe ziwawa zodza kaamba kosiyana maganizo pa ndale,” adatero a Banda.

Ndipo m’chikalata chimene adasainira mneneri wa chipani cha UTM a Felix Njawala ati ziwawa ngati zimene zidachitika ku Mpondela si zoyenera mu ulamuliro wa demokalase.

“Izi zikutikumbutsa nthawi ya kampeni ya chisankho chapitacho. Anthu ena adatitchingira pa njira pomwe timachokera ku Nsamala kupita ku Nselema. Galimoto zathu ziwiri zidaotchedwa. Ndale zoopsezana zotere n’zosafunika,” adatero iwo.

A Njawala adapempha apolisi kuti afufuze ndi kumanga amene adayambitsa ziwawazo kuti chikhulupiriro cha Amalawi ku apolisi chibwerere m’chimake.

“Dziko silingatukuke chifukwa tikuotcha galimoto za ena. Tipemphenso a MCP kuti aleke kugwiritsa ntchito apolisi popondereza ena,” atero a Njawala.

Poikirapo ndemanga, mgwirizano wa mabungwe omenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) ladzudzula ziwawa zimene zidachitika ku Dowa.

Bungweli lidapempha apolisi kuti afufuze ndi kumanga amene adachita izi. “Apolisi agwire ntchito yawo mosayang’ana nkhope pofuna kuonetsa kuti palibe amene ali pamwamba pa lamulo,” chidatero chikalata cha mgwirizanowo.

M’sabatayi, mneneri wa apolisi m’dziko lino a Peter Kalaya adati apolisi akufufuza amene adachita izi.

“Tikufufuza amene adachita izi. Sitigona ngati apolisi. Ndipo tipemphe azipani onse kuti mchitidwe wa ziwawa utheretu. Tikuyenera kukhala anthu ololerana,” adatero iwo.

Padakalipano, komishoni ya mtendere yakhala ikukumana ndi atsogoleri a zipani pa nkhani ya ziwawa. Iwo akumana kale ndi a Chakwera, mtsogoleri wa UTM a Dalitso Kabambe, Mayi Banda, mtsogoleri wa UDF a Atupele Muluzi komanso mtsogoleri wakale wa dziko lino a Bakili Muluzi.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button