DPP yasankha atsogoleri atsopano

Msonkhano wa masiku atatu wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) womwe umachitikira mu mzinda wa Blantyre wasankha mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, kuti ndiye adzatsogoleri chipanicho pa zisankho zapatatu za chaka cha mawa.

Wachiwiri kwa Mutharika m’chigawo chakumpoto ndi Goodall Gondwe, chapakati ndi Uladi Mussa,  chakummawa Bright Msaka pamene Kondwani Nankhumwa wa m’chigawo chakummwera.

Mutharika, Gondwe ndi Msaka adasankhidwa opanda opikitsana nawo pamene Mussa adagwetsa Dean Josaya Banda, Zelia Chakale, Hetherwick Ntaba ndi Samuel Tembenu pamene Nankhumwa adasosola nthenga Joseph Mwanamvekha ndi Henry Mussa.

Mlembi wamkulu wa chipanichi ndi Greselder Jeffrey, mneneri ndi Nicholas Dausi, msungichuma Jappie Mhango, mkulu wokopa anthu Everton Chimulirenji, wa zochitikachitika Symon Vuwa Kaunda, woona za chuma Ralph Jooma, wa za malamulo Charles Mhango, woona za amayi Cecilia Chazama ndipo mkulu wa zokonzakonza ndi Chimwemwe Chipungu.

Share This Post

Powered by