Nkhani

Chilima adzapikitsana nawo chaka cha mawa

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulos Chilima, wati adzaima nawo pa zisankho za chaka cha mawa dongosolo lonse loyenera posankha mtsogoleri likadzatsatidwa.

Chilima adalankhula izi pa pologalamu ya padera pa wailesi ya Zodiak Broadcasting Station (ZBS).

Zidali chonchi Mutharika ndi Chilima asadasemphane

Pa June 6 Chilima adalengeza kuti atuluka Democratic Progressive Party (DPP) kaamba ka za mtopola zomwe achinyamata achipanicho amachitira anthu amufuna kuti adzapikitsane ndi mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, pa msonkhano wosankha atsogoleri a chipanicho.

Koma Chilima adakana “kudzalimbana ndi eni ake a chipani cha DPP” ndipo m’malo mwake adaganiza zotulukamo.

Kusagwirizana kudabuka m’chipanicho kuchokera pomwe mkazi wa mtsogoleri wakale wa dziko lino, Callista Mutharika, adapempha mlamu wake, Peter Mutharika, kuti apereke mpando wake kwa Chilima kaamba koti wakula, komanso sangadzapambane pa zisankhozo.

Peter Mutharika adakana kutula pansi udindowo ndpo adati aliyense yemwe sakufuna kuti adzaimenso ndi Yudase Isikariote wosafunira DPP zabwino.

Koma polankhula ndi wailesi ya ZBS, Chilima adatsimikizira Amalawi kuti ndi wokonzeka kudzapikitsana nawo pa zisankho za chaka cha mawa dongosolo loyenera posankhira atsogoleri likatsatidwa kaamba koti sakufuna kukakamiza anthu kuti adzawaimire.

Iye adati anthu ambiri akhala akulimbikitsa kuti adzapikitsane nawo. Koma sadafotokoze kuti adzaima payekha, alowa chipani kapena ayambitsa chake.

“Tikukuma ndi mabungwe, komanso zipani ndipo dongosolo lonse likatha tilengeza zotsatira zake.

“Kuima pa wekha n’kwabwino, koma uyenera kukuganizira bwino chifukwa utha kumalimbikira mtunda wopanga madzi,” adatero mtsogoleri yemwe walongeza Amalawi kuti tsogolo la Chilima Movement lisongola pasanathe masiku 10.

Mtsogoleriyu waonetsa ubwino wa mgwirizano pakati pa zipani ngati womwe udachitika mu 2004.

Iye watsutsa zoti Mpingo wa Katolika ndiwo ukumulimbikitsa kuti adzaima. “Mpingo wa Katolika umalimbikitsa kuti Akhristu ake kuti azitenga nawo mbali pa ndale, koma sulodzera anthu mtsogoleri woti adzamuvotere.”

Chilima wakhala akupezeka, komanso kulankhula misonkhano yisiyanasiyana ya mpingo wa Katolika komwe ansembe ena akhala akumulimbikitsa kuti asakane maitanidwe wodzaima nawo pa zisankho za chaka cha mawa.

Mtsogoleriyu wakhala akudzudzula mchitidwe wa ziphuphu m’boma zomwe zakhala zikudabwitsa anthu kaamba koti iyeyo ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino.

Chilima wapempha anthu kuti akalembetse mwaunyinji wawo kuti adzaponye nawo mavoti pa zisankhozo.

“Kulumpha dzenje n’kuliwonera patali. Ndipemphe anthu kuti akalembetse chifukwa Mulungu adzawapatsa atsogoleri womwe akufuna,” adatero mtsogoleriyu.

Chilima walimbikitsanso achinyamata omwe akufuna kudzapikitsana nawo pa zisankhozo kuti asagwe mpwayi ndipo adapereka zitsanzo za andale odziwika bwino monga Aleke Banda, Gwanda Chakuamba ndi ena omwe adalowa ndale ali achinyamata.

Related Articles

Back to top button