Ena ayamba kukolola chimanga chosauma
Mbala zavuta mpaka alimi ena ayamba kukolola dowe kuopa kuti akadikira nyengo yoyenera kukolola adzapeza mapesi okhaokha m’munda.
Nduna ya za ulimi a Sam Kawale ati unduna wawo ukudziwa zimenezi koma apempha alimi omwe akukolola mondokwawo kuti adekhe.

A Kawale ati ngakhale ena akukolola poopa akuba, ena akukolola pofuna kulewa njala koma iwo ati oterowo akudzilakwira chifukwa boma lili nchimanga chokwanira kugawira anthu omwe alibe chakudya.
“Zimenezo tikuzidziwa koma nkhani yaikulu ndi yoti anthu akuopa njala. Mwa ichi, unduna wathu ukulimbikitsa anthu kuti asapupulume boma liwapatsa chimanga,” atero a Kawale.
Koma kadaulo wa z amalimidwe a Albert Changaya omwe ndi mkulu wa nthambi ya za kafukufuku wa ulimi ya Aret ati pali chiopsezo chachikulu alimi akamakolola chimanga chili chachiwisi.
A Changaya ati chimanga chikakololedwa chosauma, chikamatha madzi chimachita kafumbu ndipo ufa wake siulimba mu mtanga.
“Zangochitika kuti alimiwo akuopa kuberedwa koma zoona n’zoti mapeto ake apeza zochepa kusiyana n’zomwe akadapeza akadadekha.
“Pa za malimidwe timati chimanga chimayenera kukololedwa mapesi ndi makoko akauma chifukwa chimanga chimakhala chitamwa madzi bwinobwino. Zomwe zikuchitika apapa, chimanga chambiri chidzakhala kafumbu,” atero a Changaya.
M’buku la ulangizi wa za malimidwe achimanga, adaunikira kuti kupatula kuuma kwa mapesi ndi makoko, alimi akhoza kudziwa kuti chimanga chafikapo chikamachita visekese m’manja ofumbata.
Poonjezera ulangizi wawo, a Changaya ati kupatula kuchita kafumbu, chimanga chokolola chosauma mokwanira chimavuta kusamala kwake.
“Chimanga chakhala chikadali chanthete ndiye ngakhale kuyanika n’kuthira mankhwala, nankafumbwe savutika kuchecheta akalowa,” atero a Changaya.
Pa zomwe boma lakonza kukonzekera chomwe chingadze kaamba ka zomwe zikuchitikazo, a Kawale ati pali mapulani a pompopompo, apakatikati ndi ena amtsogolo.
“Njira ya pompopompo ndi ija ndanena kale yogawa chimanga, pali njira yachiwiri yopeleka ndalama za mtukula pakhomo ndiye pali pulogalamu ya mthilira.
“Njira izizi mukaziika pamodzi simudzamva munthu akudandaula za njala. Komabe sikuti tikugwirizana ndi zoti anthu azikolola chimanga chachiwisi,” atero iwo.
Mfumu yaikulu Chilooko ya m’boma la Ntchisi yati chimanga chikachita kafumbu, ufa wake siulimba ndipo njala siyichedwa kulowa pakhomo.
“Zangovuta kuti anthu alibe chakudya komanso ena aonamo bizinesi m’chimanga n’chifukwa chake kuba kwakula koma kunena zoona, chimanga sakolola dowe ayi,” atero a Chilooko.
Kadaulo pa za malimidwe a Tamani Nkhono Mvula ati n’kusintha kwa nyengoku komanso kuguga kwa nthaka, alimi akuyenera kumagwiritsa ntchito manyowa chifukwa chimanga sichichedwa kukhuthala.