Kwadza zipani zina za ndale
Pomwe masiku a chisankho akusunthira ku chitseko, zipani zina za ndale zitatu zalembetsa ku ofesi ya mlembi wa zipani za ndale, kufikitsa chiwerengero cha zipani pa 23.
Mlembi wa zipani za ndale a Kizito Tenthani atsimikiza za kulembetsa kwa zipanizo zomwe ndi Patriotic Citizens Party (PCP), chotsogozedwa ndi a Jordan Sauti; Solidarity Alliance Party (SA) cha a Victor Madhlopa; ndi Anyamata Atsikana Azimai Party (AAA) cha a Akwame Bandawe.

“Koma tawadziwitsa kuti akuyenera kutsatira malamulo a zipani za ndale apo ayi tili ndi mphamvu zowafufuta m’kaundula wa zipani za ndale,” atero a Tenthani.
Malamulo olembetsera zipani za ndale a 2018 amaunikira kuti gulu likhoza kulembetsa chipani ngati chili ndi mboni zokwanira, wa za malamulo komanso umboni woti gululo lili ndi olitsatira.
Kadaulo pa ndale a George Phiri adatambasula kuti zipani za ndale zimabadwa ngati gulu lina silikukhutira ndi mfundo za zipani zomwe zilipo kale, kapena pakakhala kugalukirana.
“Chipani kupeza anthu ndi mfundo zake ndiye ena akaona kuti sakukhutira ndi mfundo za zipani zina, amayamba chawo. Koma pali gulu lina limasamuka m’chipani n’kuyamba chawo kaamba kokhumudwa ndi zochitika mchipanimo,” adatero a Phiri.
Zitsanzo za zipani zoyamba kaamba kokhumudwa ndi zochitika m’zipani zawo ndi DPP yomwe idatuluka mu UDF chifukwa malemu Bingu wa Mutharika samagwirizana ndi zoti aziuzidwa zochita ndi a Bakili Muluzi.
Chaka chatha chomwechi, kudabadwa chipani cha PDP chomwe adayambitsa ndi a Kondwani Nankhumwa atawachotsa m’chipani cha DPP.
Nawo malemu a Saulos Chilima omwe adali wachiwiri kwa pulezidenti wa Malawi m’nthawi ya DPP adatuluka n’kuyamba UTM ataona kuti ku DPP sizimawayendera.
Zateremu, zikutanthauza kuti pakapanda kukhala migwirizano iliyonse, ndiye kuti pa chisankho chomwe chikubweracho padzakhala opikisana pa upulezidenti 26 kuphatikizapo atatu oima pa okha.
Malamulo a dziko lino amapereka ufulu kwa munthu aliyense kukhala gawo lachipani kapena mbali ya ndale yomwe yamusangalatsa koma kutengera zomwe zakhala zikuchitika m’dziko muno, andale ambiri amathamangira komwe aona ponona.
A Ernest Thindwa omwe ndi kadaulo pa ndale adaunikira kuti pali kusiyana pakati pa anthu a ndale ndi anthu ofuna utsogoleri.
“Ndale tikatengera patanthauzo la Chingerezi, tidatanthauzira kolakwika, dziko lino limafunika anthu ofuna utsogoleri osati andale ayi. Koma zidalakwika koyambirira komwe,” adatero iwo.
Padakalipano, zipani zagundika ndi ma pulaimale ndipo ena ayamba kale kutuluka m’zipani zawo kukalowa zina kaamba koti adagwa pa m’mapulaimale.