Nkhani

Fetereza wachinyengo wafika pamsika

Listen to this article

Pomwe mdima pa za pulogalamu ya zipangizo zotsika mtengo ya Affordable Inputs Programme (AIP) ukubalalika, tsopano palowa nkhungu ya fetereza wachinyengo.

M’mwezi wa November pomwe alimi agundika kusaka zipangizo zaulimi, fetereza wachinyengo wapezeka m’maboma a Mchinji ndi Dowa omwenso ndi ena mwa maboma odalirika paulimi.

Ena akhoza kugula fetereza wosakhala bwino

Pa 25 November 2022, apolisi a m’boma la Dowa adamanga a Glaswell Kammuoneni a zaka 38 chifukwa chopezeka ndi fetereza wachingo ndipo mneneri wapolisi ya Mponera a Macpatson Msadala atsimikiza.

“Tidalandira dandaulo kwa a Chisinsi Chunga a zaka 26 kuti fetereza wa NPK yemwe adagula kwa a Kammuoneni pamtengo wa K55 000 pa thumba adali osakaniza ndi dothi ndipo titapita kugolosale yawo tidakalanda matumba ena 11,” adatero a Msadala.

Aka n’kachiwiri mwezi umodzi chifukwa pa 7 November 2022, fetereza wina wachinyengo yemwe mudali mchenga osakaniza ndi utoto wa laimu adapezeka m’boma la Mchinji.

Mlimi yemwe adagula feterezayo adadandaula pa vidyo yomwe idatumizidwa m’masamba a mchezo kuti feterezayo sadagwire ntchito m’munda wake.

Nduna ya zaulimi a Sam Kawale adati undunawo ukudziwa za nkhaniyo ndipo akadaulo a zakafukufuku ku undunawo akufufuza za fetereza wachinyengowo.

“Akadaulo a zakafukufuku ku unduna wathu akufufuza komanso tikugwira ntchito limodzi ndi anzathu a Malawi Bureau of Standards, a Anti-Corruption Bureau ndi apolisi kuti tithane ndi akamberemberewo,” adatero a Kawale.

Koma kadaulo pa zaulimi a Tamani Nkhono-Mvula ati alimi akuyenera kuchenjera chifukwa akamberembere akudziwa kuti alimiwo ali kakasi kufuna zipangizo monga fetereza ndiye asamakopeke akamva mtengo wotsika.

“Vuto ndi loti fetereza wakwera udyo ndiye poterepa, akamberembere amabwera ndi utambwali wawo potsatsa fetereza wachinyengo motsika mtengo kuti alimi akopeke chifukwa chakusimidwa,” atero a Nkhono Mvula.

Iwo ati mpofunika kuti unduna wa zaulimi ndi makampani ogulitsa fetereza akhalirane pansi n’kukhazikitsa mtengo weniweni omwe alimi aziudziwa kuti azidabwa venda akawatsatsa fetereza wotsika mtengo.

A Nkhono-Mvula atinso mchitidwe wogulitsa fetereza wachinyengo sungathe chifukwa zolango zomwe zimapelekedwa anthuwo akagwidwa nzopepuka zosapeleka mantha kwa akamberembere.

Koma a Kawale ati pulogalamu ya AIP siyikukhudzidwa ndi fetereza wachinyengowo chifukwa ali mmalo wotetezedwa ndiponso mtengo wake udakhazikidwa kale.

“Alimi aziombola fetereza wa AIP pa mtengo wa K15 000 ndipo boma lizisonkhapo K50 000 pa thumba la makilogalamu 50 ndiye alimi asalole zosemphana ndi mtengowu” adatero a Kawale.

Iwo atinso akuyembekezera zopititsa bilu yokhudza malonda a fetereza ku Nyumba ya Malamulo ndipo biluyo ikadzadutsa idzathandiza kuthana ndi mchitidwe waukamberembere.

Chaka chatha, unduna wa zaulimi udachotsa makampani ena pamndandanda wa makampani ogulitsa fetereza wa AIP chifukwa chopezeka ndi fetereza wa chinyengo.

Malingana ndi undunawo, fetereza wachinyengoyo adapezeka m’zigawo ziwiri kummwera ndi pakati pomwe fetereza wachinyengo wapezekanso kale chaka chino.

Nduna ya kale ya zaulimi a Lobin Lowe adati kupezeka kwa fetereza wachinyengoyo n’chimodzi mwa zifukwa zomwe zidasokoneza ulimi wa chaka chatha kuti alimi ambiri asakolole moyenera.

Related Articles

Back to top button
Translate »