Nkhani

Gogo athawa m’mudzi mwake

Abale a gogo Binwell Chabwera amene adathawitsidwa pomuganizira kuti adapha mdzukulu wake m’matsenga anenetsa kuti iwo sakufunanso kuona gogoyo.

Gogo Chabwera wakhala m’manja mwa apolisi ya Zalewa m’boma la Neno kwa sabata zitatu iye atathawitsidwa kumudzi kwawo pofuna moyo wake kutsatira imfa ya mdzukulu wake.

Gogo Chabwera

Pamene timasindikiza nkhaniyi n’kuti gogoyo atatengedwa ndi akufuna kwabwino a Mai Mbambande Foundation mu mzinda wa Lilongwe.

Koma gogoyo adakana kuti iye satamba ndipo nayenso adali wodabwa kuti akumuganizira zoti ndi amene wazimitsa mdzukulu wake, Chiyembekezo Baisoni.

“Ine sinditamba, ndipo ndikadakhala ndimapanga zimenezo bwezi nditatha ana anga amene mpaka lero ali moyo,” adatero.

Ulendo ku Neno

Lachisanu masana Msangulutso udafika m’mudzi mwa Kasamba 1 kwa T/A Saimoni kwawo kwa gogoyo m’bomalo.

Kumeneko tidapeza ana 5 agogoyo omwe ndi amayi anayi ndi mwamuna mmodzi. Gogoyo amasungidwa ndi chidzukulu chake, Chifundo Switi m’mudzi omwewo.

Fasitoni Chabwera ndi mwana wake wa m’mudzi yekhayo amene ali moyo, iye adati zochita za gogoyo ndi zomwe zidapereka uthenga woipa kuti anthu amuganizire kuti ndi amene wakonza mdzukulu wakeyo.

Iye adati gogoyo adayamba pakale kunena kuti athana ndi adzukulu akewo komanso ana ake koma izi amalankhula popanda kumuyamba.

Imfa ya mdzukulu wa gogoyo ndi yomwe idachititsa abanja kuti aloze zala gogoyo kuti ndi amene wakonza.

“Sabata idatha mdzukulu wakeyo akudwala koma gogoyo sadafune kudzamuzonda. Tsiku lina tidachita kumukakamiza kuti adzamuone ndipo adabwera koma zomwe adachita zidatidabwitsa,” adatero Fasitoni.

“Podzamuonapo adati titenge chitosi cha nkhuku ndi kuchisungunula ndipo madziwo adamuwaza ku mutu ati akhala bwino koma sizidathandize,” adatero.

Iye adati pofika pa August 26 mdzukuluyo adatsanzika ndipo aliyense adaganizira kuti wachita izi ndi gogoyo.

Adaonjeza kuti abale ena sadachedwe koma kuthotha gogoyo ndipo adamuthira zikwapu achitetezo a m’mudzi asadabwere kuwalanditsa.

Fasitoni adati maliro ataikidwa aliyense adanjanja kuti azimitse gogoyo koma zidakanika chifukwa n’kuti gogoyo atathawitsidwa kale.

Mmalo mwake, anthu adakayatsa zovala za gogoyo kuphatikiza akatundu ake onse.

“Ifeyo gogoyu sitikumufunanso kuno, ngati apolisi akufuna amutulutse, ndiye apite kwina osati kuno. Akabwera kuno ndiye chomwe chidzachitike sindinena chifukwa izizi adayamba kalekale kunena kuti atikukuta,” adatero Fasitoni.

Chiyambi cha matenda

Mkazi wa malemu Sera Baisoni wa zaka 24 adati mwamuna wake amene adali ndi zaka 27 adakumana ndi ngozi tsiku lomwe adapita kuthengo kukagwetsa mitengo yoti aotchere makala.

Iye adati atapita kuthengoko, sadachedwe kubwerera pamene amati mutu wake ukumuwawa.

“Adati atangokhapa mtengo kuthengoko adangomva ngati chithu chamumenya m’mutu. Ndidakagula mankhwala koma sizidathandize.

“Pakutha pa masiku adatupa m’mutu komanso diso lidatuluka m’malo mwake. Tidathamangira ku chipatala koma sizidatheke, ndipo adamwalira,” adatero.

Iye adati chomwe akufuna n’kuti anthu ofuna kwabwino amuthandize chifukwa mwamuna wake wasiya ana awiri omwe ndi ang’onoang’ono amene sangakwanitse kuwathandiza.

Gogo Chabwera amasungidwa ndi mdzukulu wake Chifundo Switi amene wakhala nawo kwa zaka zitatu.

Kumufunsa za ufiti kwa gogoyo, Switi adati iye sadayambe wakhudzidwapo ndi gogoyo ngakhale ana ake onse 5 amene ali nawo.

“Ine nkhani ya ufiti ndimaimva kwa abale awo, koma ineyo sindinganene kuti gogoyu adayamba wandilodzapo,” adatero.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button