Nkhani

Jombo ikudiliza matimu

Listen to this article

Chalaka bakha nkhuku singatole. Linda madzi apite ndiye udziti wadala. Miyambiyi ndiyo idatsanuka m’sabatayi kaamba ka jombo yomwe idathudzula Nyerere komanso kudiriza Maule mwachipongwe.

Oyambirira kudandaula ndi jombo adali neba winayu ku Zomba kumene amati zikamuyendera. Iye adanyang’wa kuti adadya kale mkango wa umuna ndipo udatsala ndi waukazi koma awo adali maloto amasana chifukwa pakutha pa mphindi 90 kumva kuti maliro a neba ayikidwa ku Thodwe koma nkhope anthu amakaonera ku Chinamwali.

Neba winayu timati mwina zimuyendera atangothyola banki ya ku Lilongwe koma kupita pa Dedza kumvanso kuti matenda akula ndipo amugoneka pachipatala cha Dedza.

Zikatere chikho chimasiya kukoma chifukwa maso ndi zokamba za anthu zimakhala pa matimu awiriwa. Koma mmene jombo ikufikira zikukayikitsa ngati matimu enawa azifika pena ndi mipikisano yathu.

Bwanji jomboyi izisewera payokha kapena izikumana ndi anyamata oyenda ndi unyolo?

Tikuganiza kuti manebawa adakakhala ndi owathandiza bwezi akupirira ndi jombo. Koma bambo awo angomwalira dzulodzuloli ndiye sitingayembekezere kuti angalimbe pa jombo.

Mwinatu asilikaliwa thandizo la boma lomwe amapeza ndilo likuwachititsa kuti azisangalala poponda anzawo. Timaganiza kuti ku Lilongwe aneba athu kumeneko ayimitsana ndi jombo polingalira kuti iwo ndi eni ndalama koma madzi enieni.

Ayi ife tipepese anebawa pa ngozi yachitika. Tamva kuti maso anu muponyeza pa Standard Bank ndi ligi komabe ndi momwe jomboyi ikufikira ife tilibe chikhulupiriro.

Related Articles

Back to top button