Nkhani

Joyce Banda akumana ndi mafumu, otsutsa azizwa

Listen to this article
Joyce Banda akumana ndi mafumu, otsutsa azizwa
Joyce Banda akumana ndi mafumu, otsutsa azizwa

Mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda Lachinayi adakumana ndi mafumu a m’dziko muno, zomwe zidachititsa otsutsa boma ena kuzizwa.

Banda adakumana ndi mafumuwo kunyumba ya boma ya Sanjika mumzinda wa Blantyre.

Koma mneneri wa chipani cha UDF Ken Ndanga adati chipanicho chakhala chikudabwa ndi momwe Banda amachitira zokhudza mafumu.

“Tikudziwa kuti iyi ndi njira yakuti mafumu akhale mbali yake pomwe chisankho chili pamphuno,” adatero Ndanga.

Ndipo mneneri wa DPP Nicholas Dausi adati akudabwa kuti Banda akuchita zimene ankadzudzula nazo mtsogoleri wakale wa dziko lino Bingu wa Mutharika.

“Bingu akaitana mafumu, Banda amati si bwino. Mmalo mowasiya mafumu kuunikira momwe kalembera wa chisankho akuyendera, akuwaitanitsa kunyumba ya boma,” adatero Dausi.

Pomwe timasindikiza Tamvani Lachinayi n’kuti zisanadziwike kuti Banda ndi mafumuwo amakambirana chiyani.

Mneneri wa kunyumba ya boma Steven Nhlane, adanena msonkhanowo usadachitike kuti samadziwa zomwe mtsogoleri wa dziko lino ndi mafumuwo amakambirana.

Naye mneneri wa unduna wa maboma aang’ono Maganizo Mazeze samadziwa zomwe amakambirana.

Related Articles

Back to top button
Translate »