Nkhani

K34.8 biliyoni ya ngozi zadzidzidzi

Nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya DoDMA yatolera K34.8 biliyoni ya ngozi zogwa mwadzidzidzi koma ndalamazo n’zochepa poyerekeza ndi kukula kwa ngozizo.

M’miyezi ya February ndi March 2022 Amalawi ambiri adazunzika ndi ngozi za namondwe wa Ana komanso Gombe ndipo nthambi ya DoDMA idali pachipsinjo chosamalira anthu okhudzidwawo.

Nyumba ndi katundu zambiri zidawonongeka ndi Anna komanso Gombe

Polankhula ndi .Tamvani Lachitatu, mkulu wa DoDMA a Charles Kalemba adati nthambiyo idatolera ndalama komanso katundu okwana K34.8 biliyoni.

Koma nthambiyo imafunika ndalama zokwana K72.7 biliyoni kuti ikwanitse kuthandiza anthu 166 000 omwe adakhudzidwa ndi ngozizo.

“Panopa tili mkati motolera thandizo pamodzi ndi mabungwe komanso anzathu akufuna kwabwino. Ife sitimasangalala kuona anthu akuzunzika chifukwa cha ngozi zogwa mwadzidzidzi,” adatero a Kalemba.

Koma mneneri wa nthambiyo a Chipiliro Khamula adapereka chiyembekezo ponena kuti anthu ambiri omwe adakhudzidwa akuchoka m’misasa n’kumabwerera kwawo.

“Iyiyi ndi nkhani yabwino kwambiri chifukwa zikuonetsa kuti anthu ambiri omwe adali m’mavuto panopa akupepukidwa ndipo tikuyembekeza kuti omwe atsalawo nawo zinthu ziwasinthira,” adatero a Khamula.

Mfumu yayikulu Mlonyeni ya ku Mchinji yomwe dera lake lidakhudzidwa ndi ngozizo yati ndi yokondwa kuti tsogolo layamba kuoneka pa thandizo la anthu omwe adakhudzidwa.

Iwo ati anthu kuderalo adali manja m’khosi ngoziyo itagwa ndipo mafumu adali pachipsinjo kusowa kolowera kuti anthuwo apeze mpumulo.

“Ngati pali nthawi yowawa ndi pangozi zogwa mwadzidzidzi chifukwa anthu amakhala pamavuto oopsa. Nanji ife mafumu timakhala pachipsinjo zowopsa moti nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi yagwira ntchito yotamandika,” atero a Mlonyeni.

Anthu omwe ngozizo zidawakhudza akusoweka zambiri monga zovala, pogona, zofunda ndi chakudya zomwe DoDMA ndi mabungwe ena akuyenera kuthandizapo.

Mmodzi mwa akuluakulu ku bungwe la Malawi Red Cross Society a Gumbi Gumbi adati bungwe lawo likuyesetsa kuthandiza anthu okhudzidwawo koma adati n’zomvetsa chisoni kuti anthu ena akalandira thandizolo akugulitsa.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button