Nkhani

K5 000 yayamba kugwira ntchito

Listen to this article

Ndalama yatsopano ya K5 000 idayamba kugwira ntchito Lachinayi pa 24 February 2022 koma Amalawi ena akuda nayo nkhawa kuti malonda azivuta komanso ena akuti ukataya ndalama imodzi ndiye kuti wataya zambiri.

A John Macheso omwe amayendetsa minibasi mumzinda wa Lilongwe ati ndalama ya K5 000 ndi yovuta kusintha makamaka operekayo akakhala woyenda ulendo waufupi umene akuyenera kulipira ndalama zochepa.

“Ndiye tikulingalira kuti anthu anayi apereke K5 000 aliyense koma akuyenda mtunda wosakwana K500 chenje ungachitenge kuti munthu ngati imavuta K2 000 yeniyeniyi? Zifukwa zawo zotulutsira ndalamayo nzomveka koma bizinesi ivuta,” atero a Macheso.

Nawo mayi Sunganani Mwachumu omwe bizinesi yawo ndi yogulitsa nthochi ati ndalamayo ikhoza kupeleka danga kwa anthu achipongwe ofuna kudya malonda a anzawo mwaulere.

“Ena amachita dala kudya nthochi za K200 n’kupereka ndalama yaikulu cholinga ikakuvuta chenje uwasiire kuti adzakupatsa tsiku lina ndiye ndi K5 000 imeneyi atidyeradi atero a Mwachumu.malonda aulele,”

Bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) lati likudera nkhawa alimi kuti akambelembele akhoza kuwabera powagula mbewu ndi ndalama zachinyengo pozindikira kuti alimi ambiri sadazolowere zizindikiro za ndalama yatsopanoyo.

“Pakufunuka kuchilimika kuphunzitsa alimi za ndalamayo kuti azitha kusiyanitsa ndalama yeniyeni ndi chizude apo ayi chaka chino tikhoza kumva madandaulo ambiri kuchoka kwa alimi kuti abeledwa,” adatero mkulu wa FUM a Jacob Nyirongo.

Mkulu wa banki ya Reserve Bank of Malawi a Wilson Banda adalengeza kuti atulutsa K5 000 yomwe ikhale ndalama yaikulu kwambiri komanso asintha zizindikiro za pa ndalama ya K2 000 zimene zidayamba kugwira ntchito Lachinayi.

Mneneri wa bankiyo a Ralph Tseka adati K2 000 yatsopanoyo izigwira ntchito limodzi ndi yakale kwa nyengo kenako yakaleyo idzatha ntchito.

Iwo adati uthenga wa zizindikiro za ndalamazo ukuperekedwa kudzera m’manyuzipepala, makanema ndi m’mawailesi ndipo akukhulupirira kuti uthengawo wafika paliponse.

“Takhala tikuika m’manyuzipepala ndi m’mawailesi kwa kanthawi tsopano. Kukakhala kuthetsa K2 000 yakale, tizipanga pang’onopang’ono momwe zimakhalira nthawi zonse zizindikiro za ndalama zikasintha,” adatero a Tseka.

Pothirirapo ndemanga, wolankhulira chipani cha Democratic Progressive pa zachuma a Joseph Mwanamvekha adati kubweretsa ndalama zatsopano kumabwera ndi mavuto ake.

“Maiko ambiri omwe ali ndi ndalama zikuluzikulu, ndi omwe chuma chawo sichiyenda bwino komanso zimapangitsa kuti anthu azizembetsa ndalama mosavuta komanso azithawa misonkho,” adatero a Mwanamvekha.

Ndipo mkulu wabungwe loyimira anthu ogula katundu la Comsumers Association of Malawi (Cama) a John Kapito nawo adati kutulutsa ndalama yaikuluyo zikusonyeza kuti chuma sichikuyenda bwino.

“Basi tingovomera kuti ndalama yathu yatha mphamvu, muzikumbukira momwe zidakhalira ku Zimbabwe zaka za mmbuyomo,” adatero a Kapito.

Koma a Banda adati ndalama yaikulu imathandiza kuti anthu asamavutike kunyamula ndalama zankhaninkhani pokagula katundu chinthu chomwe chimaonjezera chitetezo pa ndalama zawo.

Woyang’anira za ndalama ku Reserve Bank of Malawi a Muopeni Ngwalo adati pa K2 000 achotsapo chithunzi cha sukulu ya ukachenjede ya Must chomwe chikuimirira kutukula maphunziro ndipo aikapo khothi la majisitileti ya ku Blantyre kuimirira nkhondo yolimbana ndi katangale.

Related Articles

Back to top button