Kafukufuku wa chamba watha

Zotsatira za kafukufuku wa ulimi wa chamba zomwe Amalawi akhala akudikira zatuluka koma mlembi wa unduna wa zamalimidwe, mthilira ndi chitukuko cha madzi Gray Nyandule Phiri wati zotsatirazi akuzisunga mwachisinsi.

Phiri wati zotsatirazi zomwe kafukufuku wake watha zaka zitatu ziyamba zapita ku ofesi ya presidenti ndi nduna zake (OPC) kuti akaziunike zisadaulutsidwe kwa Amalawi.

“Kafukufukuyu adatenga zaka zitatu ku Chitedze ndi ku Salima ndipo zotsatira zake zatuluka tsopano koma tikudikira kuti akaziunike ku OPC kenako tidzazitengere ku Nyumba ya Malamulo,” adatero Nyandule Phiri.

Phungu wa dera la kumpoto kwa Ntchisi Boniface Kadzamira ndiye adabweretsa nkhani yololeza kulima chamba m’Nyumba ya Malamulo zaka zitatu zapitazo ndipo aphungu adavomereza nkhaniyi atakambirana.

Akadaulo osiyanasiyana akhala akuthirira ndemanga za kufunika kothamangitsa kafukufukuyu kuti dziko la Malawi liyambe kulima n’kugulitsa chamba chomwe ena akuti chikhoza kusintha chuma cha dziko lino.

Katswiri wina wa bizinesi yokhudza malonda a chamba wa ku Canada wa Green Quest Pharmaceuticals adati chamba chili ndi mtengo wabwino pamsika wa maiko ndipo chikhoza kubweretsa ndalama zambiri mdziko.

Chamba chomwe akadaulowa akulimbikitsa ndi chomwe amagwiritsa ntchito m’mafakitale popanga zinthu zosiyanasiyana monga mankhwala ndipo akatswiri amati mphamvu zake n’zochepa poyerekeza ndi chamba chosuta chija chimazunguza bongo.

Polankhula ndi Tamvani, mlembi wa nthawi yoona za mbewu zogwiritsidwa ntchito mmafakitale Industry Crops Association (ICA) Hellen Chabunya adati boma likuyenera kukhala ndi chidwi pa kafukufuku wa ulimi wa chamba kuti dziko lino litukuke.

“Chongofunika apa nkuwonetsetsa kuti tapanga malamulo ogwira okhudza kayendetsedwe ka ulimi ndi malonda a chambachi. Zina mwa izi nkuwonetsetsa kuti taunikaso malamulo ena okhudza mbeu ngati zimenezi,” adatero Chabunya.

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.