‘Kamuzu adali chitsime chakuya’
Pomwe Amalawi lero pa 14 May akukumbukira moyo ndi utsogoleri wa mtsogoleri woyamba a Hastings Kamuzu Banda, mizwanya pa mbiri ya dziko lino yati Kamuzu ndi chitsime cha ndale.
Chaka chilichonse patsikuli Amalawi amakumbukira Kamuzu, amene adaphwanya chitaganya cha Angerezi cha Rhodesia ndi Nyasaland komanso kuti Amalawi apeze ufulu wodzilamulira mu 1964. Iwo adalamula dzikoli mpaka mu 1993 pomwe a Bakili Muluzi adasankhidwa pampandowo.
Koma mzwanya pa mbiri ndi zosiyiridwa kusukulu ya ukachenjede ya Mzuzu University, a Mwayi Lusaka ati chaka chino pokondwerera tsikuli, Amalawi azilingalira kuti ndale za m’dziko muno zimalondolabe mapazi a Ngwazi.
Iwo ati ngakhale atsogoleri omwe akulamula kapena akulingalira zodzalamulira asakhale ndi mawanga a a Kamuzu, iwo amayesetsa kukokerako chithunzithunzi cha a Kamuzu kumbali yawo m’njira zina.
“Mudzaona kuti ena akubweretsa ndendende zomwe a Kamuzu ankachita pomwe ena amangowonetsera kuti akupereka ulemu kwa a Kamuzu. Zonsezi n’kufuna kuti ulamuliro wawo ulemelere chifukwa a Kamuzuwo n’chitsime cha ndale,” atero a Lusaka.
Iwo ati pachifukwachi, wandale yemwe angaonetsere kotheratu kuti sangatengereko nzeru iliyonse kwa a Kamuzu akuyenera kungoiwala zoti ndale zakezo zingamutengere ku ulamuliro.
Naye kadaulo pa mbiri ya Malawi a Octavian Kadzitche ophunzitsa za mbiri ku Yunivesite ya Katolika (Cunima) ati a Kamuzu ndi woyenera kukumbukiridwa tsiku la lero chifukwa adamanga maziko wolimba a dziko lino.
Iwo ati chifukwa cha masomphenya awo komamso kulimba mtima kwawo, a Kamuzu adakwanitsa kumanga Amalawi pamodzi ndi kuwalimbikitsa pochita chitukuko mpaka dziko limaoneka komwe limalowera.
“Ndikhoza kuwafotokoza a Ngwazi ngati munthu yemwe adali woona patali pomanga dziko la Malawi. Nthawi imeneyo m’boma mudalibe zawedewede pogwira ntchito ndipo katangale kudalibe, adamanga maziko omwe sadzaonekanso m’boma.
“Kale kudalibe makompyuta koma anthu malipiro amalandira tsiku lake, apolisi amakwanitsa kukhazikitsa bata popanda mfuti kapena utsi okhetsa misozi chifukwa a Kamuzu adamanga kale maziko wolimba. Zambiri adaikiratu maziko woti akadagwira ntchito mpaka lero,” adatero a Kadzitche.
Iwo ati chokhacho choti a Kamuzu adakwanitsa kuluzanitsa Amalawi komanso kuti munthawi yawo alimi ankapindula, ntchito za mafakitale zinkayenda komanso boma lidali ndi mafakitale akeake momwe anthu akamaliza maphunziro amakalowa ntchito, n’chokwanira kukumbukira tsiku lawo.
Iwo atinso polingalira masomphenya omwe a Kamuzu adali nawo, akadakhalako lero bwenzi dziko lino likupha makwacha kuchoka m’misika ya mbewu monga soya ndi nandolo zomwe maiko akunja akufuna koma sitikwanitsa kukhutitsa msikawo.
“Ndikukhulupiriranso kuti mwina bwenzi pano tili ndi mafakitale opanga zinthu zosiyanasiyana chifukwa iwo adali ataiyamba kale ntchito imeneyo koma atsogoleri owatsatira adalephera kuipitiriza,” atero a Kadzitche.
A Kadzitche ati Amalawi akuyenera kukumbukira a Kamuzu chifukwa akadakhalapo sibwenzi maiko ena atatenga Malawi ngati kumtaya kwa katundu wosalimba ndi ntchito zomangamanga zawedewede.
Nawo a Nicholas Dausi omwe adakhala nthawi yaitali pafupi ndi a Kamuzu ati tsikuli ndi lofunika kwambiri chifukwa limakhala ngati chikumbutso cha masomphenya omwe adaunikira dziko lonse.
Iwo ati a Kamuzu adali nkhwantha pachilichonse chomwe ankachita ndipo ankalimbikitsa Amalawi kuti akafuna kuchita chinthu azitero ndi mphamvu komanso nzeru zawo zonse.
A Dausi ati palibe ulemu waukulu komanso chithokozo chomwe Amalawi angapereke kwa a Kamuzu kuposa kumawakumbukira patsiku ngati la lero.