Nkhani

Kolera yaluma mano

Listen to this article

 

Nthenda ya kolera imene idayamba ngati njerengo mwezi wa November chaka chatha, ikukwererabe moti kuchoka Lachisanu sabata yatha chiwerengero cha anthu odwala nthendayo chidachoka pa 420 kufika pa 459 Lachiwiri.

Malinga ndi zikalata zochokera ku Unduna wa Zaumoyo, anthu 6 amwalira ndi matendawa ndipo anthu 14 akulandira thandizo m’malo apadera amene undunawo udakhazikitsa m’maboma ena. Matendawa akhudza maboma a Karonga, Kasungu, Dowa, Nkhata Bay, Lilongwe, Salima, Mulanje, Nsanje, Chikwawa, Likoma, Rumphi ndi Blantyre.

Matendawa adafala ndi msodzi wina, amene adaitenga ku Wiliro m’boma la Karonga ndipo adafika nayo ku Ngala, kumene asodzi amafikira ndi kugulitsa nsomba zawo. Msodziyo adafika padokopo ali wefuwefu ndipo adachita chimbudzi mphepete mwa nyanja.

Malinga ndi Idah Msiska, yemwe ndi wapampando wa komiti ya chitukuko ya m’mudzi mwa Muyereka ku Ngala, matendawa adafala kwambiri chifukwa cha kusowa zimbudzi komanso utchisi wa deralo.

“Wodwala woyamba adafika pagombe n’kuchita chimbudzi ndipo tizilombo tidafalikira m’madzi. Chovuta china n’choti nsomba zimaola kwambiri kumalowa ndipo zimaitana ntchentche zomwe zimafalitsa matendawa. Padakalipano tikuyendera khomo ndi khomo kuti tithane ndi matendawa ndipo amene sakutsatira malangizowa amakumalipa chindapusa,” adatero Msiska.

Iye adati chodziwikiratu kuti matendawa afala chifukwa ena amachita chimbudzi m’nyanja momwe enanso amatunga madzi ogwiritsa ntchito pakhomo.

Malinga ndi mmodzi mwa anthu 258 amene apezeka ndi matendawa ku Karonga, Baxter Nyondo, matendawa ndi wovuta ndipo akungoyamika Mulungu kuti akadali moyo. Iye Lachiwiri tidamupeza akulandira thandizo pachipatala chaching’ono cha Ngala.

“Sindinkadziwa chinkandichitikira. Ndinkangothulula osalekeza. Pano bola. Ndikuyamika chifukwa achifundo adanditengera kuchipatala msanga,” adatero iye.

Iyi ndi nkhani yolingana ndi yomwe adatambasula Mercy Kachepa yemwe ankadikirira mbale wake pamalo a padera a odwala kolera ku Bwaila ku Lilongwe.

“Adafika kunyumba kuchoka kosewera akudandaula m’mimba. Posakhalitsa adayamba kugudubuka, uku akudziyipitsira. Kupanda kuikapo mtima akadapita,” adatero Kachepa.

Lolemba Nduna ya za Umoyo Atupele Muluzi idakayendera malowo komwe adatsimikiza kuti zinthu zaipa.

“Nkhondo ndiye ikumenyedwa kuti vutoli lithe koma kunena zoona, matendawa atikakamira ndipo liwiro lomwe akufalira likuopsa kwambiri,” adatero iye.

Muluzi adauza Nyumba ya Malamulo sabata yatha kuti katemera wa kolera yemwe boma likupereka akhoza kuthandiza kuthetsa kufala kwa matendawa ataperekedwa m’madera ambiri makamaka omwe ali pachiopsezo.

Oyang’anira ntchito za umoyo m’maboma a Lilongwe ndi Karonga kumene kolera yafala kwambiri, adati sakugona tulo kaamba ka matendawa.

Woyang’anira ntchito za umoyo m’boma la Lilongwe, Alinafe Mbewe, adati vutoli lakula kwambiri kwa Mitengo ku Area 36 ndi Kauma komwe anthu ambiri omwe apezeka ndi matendawa amachokera.

“Zinthu sizikusintha kwenikweni koma tikuyesetsabe. Kuchoka pa 28 December, 2017 kudzafika pa 23 January, 2018, anthu 35 ndiwo adapezeka ndi kolera koma kuchoka pa 24 January kudzafika pa 12 February, anthu 82 ndiwo apezeka,” adatero Mbewe.

Ndipo Dr Phinias Mfune ku Karonga wati vutoli likukula chifukwa tsiku lililonse pakupezeka munthu mmodzi wotenga nthendayi.

Related Articles

Back to top button