Nkhani

Kuli ziii! Pa za mthandizi

Listen to this article

Kwangoti zii! Nkhawa yagunda ngati ntchito za mthandizi zomwe anthu amalandira kangachepe akalima msewu ichitike popeza nthawi yake yadutsa osamvapo kanthu.

Iyi ndi ndondomeko yomwe anthu amalima misewu ndi kulandira ndalama yomwe imathandiza nthawi ya njala. Chaka chilichonse ntchitoyi imachitika mu January ndi February.

Koma pano miyezi itatu yatha mwachinunu, osamva kanthu kuchokera kuboma. Izi zadabwitsa mafumu amene amakhudzidwa ndi ntchitoyi pomemeza anthu a m’midzi yawo kuti akalambule misewu.

Mfumu Kabunduli ya m’boma la Nkhata Bay yati njala ikukuta anthu a m’dera lake amene amapindula ndi ntchitozo.

“February ndi mwezi wa njala, chaka chino anthu akutuwa ndi njala chifukwa cha ng’amba. Timadalira kuti tipezako mpumulo tikayamba kulima misewu koma mpaka lero,” idatero mfumuyo.

Koma mkulu woona momwe ntchito zachitukuko zikuyendera kunthambi ya Local Development Fund (LDF), Booker Matemvu, wati ntchitoyi yasintha kusiyana ndi zaka zonse.

“Ntchitoyi iyamba mu September ndipo idzatha November chaka chino. Iyi ndi nthawi yomwe takonza kuti anthu adzayambe kulima misewu,” adatero Matemvu.

Ganizoli likudabwitsa Kabunduli. “Asinthiranji? Kapena zalowa ndale? Chifukwa mwezi wa njala ndi February mpaka March. Apapa ndiye kuti asokonezeratu cholinga cha ndondomekoyi,” adatero iye.

“Tili ndi anthu kumudzi amene alibe chilichonse, ganyu ndi wovuta kumupeza ndipo amadalira kulima misewu kuti apeze thandizo. Popezera ndalama ndi ntchito yomweyi, ndiye akusinthanso?”

Matemvu wati kusinthaku kwachitika chifukwa zimatenga nthawi yaitali kuti anthu alandire ndalama zawo akalima misewu mu February.

“Pena zimafika April anthu asadalandire, n’chifukwa chake tasintha. Komanso dziwani kuti m’midzimo tayambitsa ntchito zina zomwe anthu akugwira polandirapo ndalama monga kubwezeretsa zachilengedwe,” adatero Matemvu.

Iye adati akukambirana ndi boma kuti ndondomekoyi ichitike monga imachitikira zaka zonse chifukwa cha anthu amene akutuwa ndi njala.

“Talandira madandaulo kwa anthu, maka a m’madera amene akhudzidwa ndi njala. Ngati zonse zingathe bwino ndiye kuti ntchitoyi itha kuyamba nthawi iliyonse September asadafike,” adatero Matemvu.

Ngakhale ntchitoyi idzayambe mu September monga momwe Matemvu akunenera, madera ambiri misewu ndi yoonongeka chifukwa cha mvula pamene ina ndi yosalambulidwa.

Ndalama zolimitsira misewuyi zachoka ku World Bank.

Nthambi ya LDF yomwe imayendetsa ndondomekoyi idalandira kale K97 biliyoni (132 miliyoni dollars) kuti zigwire ntchito mpaka chaka chamawa.

Njala yakhudza maboma a Neno, Nsanje, Chikwawa, Balaka, Mwanza, Phalombwe, Ntcheu, Blantyre, Karonga ndi ena.

Related Articles

Back to top button