Nkhani

Kupewa moto mu Dzalanyama kuteteza madzi

Listen to this article

Anthu ozungulira nkhalango ya Dzalanyama m’maboma a Lilongwe ndi Mchinji awapempha kuti apewe kuyambitsa moto mwachisawawa kuti ateteze ndi kusamalira zachilengedwe m’deralo.

Kudzera m’ndondomeko ya Conservation and Sustainable Management of Dzalanyama Forest Reserve (Cosma–DFR), nthambi ya za nkhalango yalimbikitsa ntchito yoteteza nkhalango ya Dzalanyama kuti zachilengedwe zibwezeredwenso m’nkhalangoyo zimene zithandizenso kuti kapezekedwe ka madzi kakhale kodalilika.

Dzalanyama Forest

Kuchulukana kwa anthu okhala mozungulira nkhalango ya Dzalanyama komanso mumzinda wa Lilongwe, kukula kwa ntchito za mafakitale kuphatikizapo kusadalilika pa kagwedwe ka mvula ndi zina mwa zifukwa zimene zikuika pachipyezo nkhalangoyi komanso  kapezekedwe ka madzi mu mzindawu kotero mabungwe ndi nthambi zosiyanasiyana za boma zikuyenera kugwirana manja kupeza njira zochepetsera vutoli.

Kafukufuku waposachedwapa anapeza kuti chilengedwe m’madera ambiri ku  nkhalango ya Dzalanyama, chinaonongeka podula mitengo zimene zapangitsa kuti nthaka yambiri ikokolokere mumtsinje ndi kukakwilira damu la Malingunde. Zinyalala zikupitilira kutaidwa mwa chisawawa komanso anthu ambiri atsekula minda mphepete mwa nkhalangoyi zimene zathandizira pa kuonongeka kwa chilengedwe.

Pamwambo wozindikiritsa anthu kuopsa kwa moto ku chilengedwe umene unachitikira m’mudzi mwa Mkokoto ku Lilongwe, Moses Njiwawo amene amayendetsa ntchito za pulojekitiyo anadandaula ndi kuchuluka kwa moto umene ukuononga chilengedwe m’nkhalango ya Dzalanyama kuphatikizaponso kukwiririka ndi kuchepa kwa madzi m’damu la Malingunde.

Pulojekitiyo ikuyembekezekanso kupindulira kampani ya Lilongwe Water Board limene limapopa madzi kuchokera a m’madamu a Kamuzu 1 ndi 2 ku Malingunde. Kaamba ka matope ochuluka amene akudza chifukwa cha kukokoloka kwa nthaka, zapangitsa kuti madzi akhale ochepa komanso kulitengera bungweli ndalama zochuluka pa mankhwala amene limagwiritsa ntchito potsukira ndi kusefa madziwa zimene zapangitsa madzi azigulitsidwa pa mtengo okwera.

Mkulu wofalitsa nkhani ndi kuphunzitsa anthu m’pulojekitiyo, Charles Gondwe, adati posachedwapa pachitika kafufuku wotsimikiza kukula kwa malo amene anakhudzidwa ndi moto m’nkhalangoyi chifukwa zithunzi za mlengalenga kudzera pa makina a nternert zikuonetsa  kuti malo ambiri a nkhalango ya Dzalanyama munatenthedwa.

Mfumu Masumbankhunda idayamikira boma la Japan kaamba ka thandizo limene likupita ku nthambi ya za nkhalango pa chilinganizo cha Cosma—DFR zimene zotsatira zake zipindulira anthu okhala mozungulira nkhalangoyi.

Related Articles

Back to top button
Translate »