Nkhani

Mvula yayandikira, makuponi kulibe

Pamene ndondomeko yogawa makuponi imayembekezeka kutha dzulo, Tamvani m’sabata ikuthayi idapeza kuti madera ena ndondomeko yolemba olandira komanso kugawa makuponi idali isadayambe.

Mneneri mu unduna wa zamalimidwe Pricilla Mateyu wati unduna wake ulengeza chomwe chichitike m’madera amene makuponi sadafike.

Tamvani yapeza kuti m’maboma ena monga Mzuzu, Mzimba, Kasungu, Salima, Dedza, Ntcheu komanso Blantyre alimi sadalandirebe makuponi.

Izi zikutsutsana ndi mawu a nduna ya zamalimidwe Kondwani Nankhumwa amene adalankhula pa 15 October ku Migowi m’boma la Phalombe pamene amakhazikitsa ndondomekoyo.

Nankhumwa adati akufuna pulogalamu ya chaka chino ikhale ya chilungamo komanso yachangu. “Pachifukwachi, kugawa makuponi kuchitika sabata ziwiri zokha.”

Mateyu Lachiwiri adatsindika mawu a Nankhumwa: “Ndi zoona, ndondomeko yogawa makuponi ikutha sabata ino.”

Mateyu adati akuyenera kufufuza kaye chomwe chalepheretsa kuti madera ena asalandire. Pofika Lachitatu, iye adali asanayankhe za madera amene sanalandire makuponiwo.

Izi zikudabwitsa kadaulo pa zaulimi Tamani Nkhono-Mvula amene wati uku ndi kusokoneza alimi.

Iye adati boma likuoneka kuti silidakonzeke, zomwe ndi zodabwitsa chifukwa amadziwa kale kuti ndondomekoyi idzakhalapo chaka chino.

“Boma limadziwa kuti chaka chino tidzakhala ndi ndondomekoyi kodi adali asadakonzeke? Tsono taonani nthawi zino koma kalembera sadachitike ndiye anthu adzalandira liti makuponi? Boma lidziwe kuti alimi alibe nthawi,” adatero.

Mfumu yaikulu Chilowamatambe ya m’boma la Kasungu yati kumeneko palibe chikuchitika pa nkhani ya makuponi.

“Kunoko ngakhale kalembera weniweniyu sitidayambe. Sitikudziwa vuto lake,” adatero.

Nayo mfumu Mabilabo Jere ya m’boma la Mzimba yati kumeneko ntchitoyi sidayambe. “Mwina tidikirebe, koma kalembera ndiye wachitika kwa omwe alandire zipangizozo,” adatero iye.

M’maboma a Ntcheu ndi Dedza nakonso akuti kulibe chachitika. Koma m’boma la Mwanza ndiye makuponi ayamba kugawidwa.

Mfumu Kanduku yati anthu amayembekezera kulandira makuponi Lachitatu. “Zonse zikatheka ndiye kuti pofika Lachisanu [dzulo] zonse zikhala zatheka,” adatero.

Ku Blantyre nakonso palibe chikuchitika. Mfumu Mbayani ya kwa T/A Makata yati mndandanda wa anthu amene alandire zipangizozo udafika kale koma makuponi sadafike.

“Zikuonetsa kuti ndi Blantyre yense anthu sadayambe kulandira makuponi,” adatero.

Malinga ndi Nankhumwa, kugawa makuponi kukatha sabata ino, anthu ayambiratu kulandira zipangizo zotsika mtengozo ndipo aliyense alandira zipangizo December asadathe.

Iye adati boma lapeza kale matani 90 000 a feteleza, matani 4 500 a mbewu ya chimanga, matani 30 a mapira, matani 50 a mpunga komanso matani oposa 900 a mbewu za gulu la nyemba.

“Makuponi onse afika kale m’dziko muno. Izitu zasiyana ndi zaka zonse chifukwa makuponi amafika mvula yoyamba itagwa kale,” adatero Nankhumwa.

Alimi 900 000 ndi amene apindule ndi ndondomekoyi ndipo thumba lolemera ndi makilogamau 50 la feteleza aziligula K4 500.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button