Nkhani

Kutentha kwa mnanu kunkira

Listen to this article

Nthambi ya za nyengo ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yati kutentha kwa mnanu komwe kwakhala kuoneka m’madera ambiri kunkira mpakana sabata ikudzayi.

Mkulu wa nthambiyo a Lucy Mtilatila ati pa chifukwachi, mbiyang’ambe zichepetse kamwedwe ka bibida chifukwa sagwirizana n’kutentha ndipo akhoza kuwapha mosavuta.

Nthambi ya zaumoyo yalangiza anthu kupewa mowa

“Chakumwa cha ukali chimayamwa madzi m’thupi ndiye m’thupi mopanda madzi n’kutentha koonjeza sizigwirizana chifukwa thupi limafuna madzi kuti zambiri zizigwira ntchito,” atero a Mtilatila.

A Mtilatila ati kalosera sakuona kusintha kulikonse kwa nyengo yotenthayi msanga kotero ati anthu azionetsetsa kuti akumwa madzi ochuluka pa tsiku kuti m’matupi mwawo azikhalamo okwanira.

Iwo atinso anthu achepetse kukhala pa dzuwa nthawi yaitali komanso kuti poyenda aziyesetsa kufunda mwafuli ndipo pa kavalidwe ati kuvala mwa ulingaombe kukhoza kuonjezera chiopsezo kwa munthu.

“Magulu ena monga ana ndi okalamba aziyang’aniridwa bwino pa nyengo imeneyi chifukwa ndiwo ali pachiopsezo chachikulu ku nyengo yotentha moonjezayi,” iwo adatero.

Malingana ndi chikalata chomwe nthambiyo idatulutsa cholosera nyengo, madera a ku chigwa cha Shire ndiwo atenthe kwambiri kumafika 42°c motsatana ndi madera a mphepete mwa nyanja omwe azifika 38°c ndipo madera ena azifika 36°c.

Kutenthaku komwe sikudasiye dera kukumanyanya masana kuyambira m’ma 11 Koloko mpakana m’ma 3 koloko nthawi yomwe anthu amakhala otanganidwa ndi ntchito zosiyanasiyana.

Kdaulo pa zachilengedwe a Mathews Malata adachenjeza kuti momwe anthu akuonongera chilengedwe monga nkhalango komanso kusasamala kataidwe ka mapulasitiki ndi zinthu zomwe siziola asamadabwe akamakumana ndi nyengo zodabwitsa.

“Nyengo zodabwitsa tikukonza tokha chifukwa chosasamala chilengedwe. Nkhani yakusintha kwa nyengo ikulengezedwa tsiku ndi tsiku ndipo zochititsa izi ndi zotsatira zake zikulengezedwa koma sitikusintha,” adatero a Malata.

Related Articles

Back to top button