Nkhani

‘Lingalirani bwino musanathane ndi fodya’

Listen to this article

Akatswiri komanso alimi ati dziko la Malawi likuyenera kulingalira mozama lisadagonjere khumbo la bungwe la zaumoyo padziko lonse la World Health Organization (WHO) pa nkhani ya malonda a fodya.

Bungwe la WHO lili pa kampeni yolimbana ndi mchitidwe osuta fodya zomwe zikutanthauza kuti kampeniyi ikadzatheka, mayiko omwe amadalira malonda a fodya ngati Malawi adzapeze njira zina zopezera chuma.

Dziko lonse lapansi likhala likukumbukira tsiku lolimbana ndi mchitidwe osuta fodya pa 31 May ndipo mutu waukulu udzakhala kulingalira mavuto omwe kusuta kumabweretsa ku mtima wa munthu.

Unduna wa zaumoyo wati umagwirizana kwatunthu ndi kampeni yolimbana ndi mchitidwe osuta fodya moti uli kalikiliki kukambirana ndi nthambi zina za boma kuti zimvetsetse ubwino wa kampeniyi.

“Ngati unduna, sitikuyenda tokha ayi tikuyendera limodzi ndi maiko anzathu komanso mabungwe ngati la WHO pa nkhani imeneyi ndipo tikugwirizana nayo kwathunthu,” watero Joshua Malango mneneri wa undunawu.

Koma katswiri wa zachuma Dalitso Kubalasa yemwenso ndi wamkulu wa bungwe lowona za momwe chuma chikuyendera la Malawi Economic Justice

Network (Mejn) wati pakufunika kulingalira mwakuya potsatira kampeniyi.

Iye wati ngakhale kampeniyi idayamba kale, fodya akadali nsanamira ya Malawi pa chuma chake komanso maziko a Amalawi ambiri makamaka m’midzi kotero tsogolo la dziko komanso Amalawi lagona pa zomwe boma lingatsate.

“Tikati tibwerere mmbuyo, tiona kuti fodya ndiye wakhala akutibweretsera chuma chambiri ndipo ndi mbewu yomwe sitingangoti lero ndi lero basi tiyisiye. Na pankhani ya chuma cha dziko lathu, kumeneko n’kudzikhweza,” adatero Kubalasa.

Iye waunikira kuti fodya yekha amabweretsa K25 pa K100 iliyonse imene boma limapeza munjira zosiyanasiyana kuphatikizapo thandizo lochoka

kunja ndipo kuti anthu ambiri amapeza chochita mu fodya.

“Padakali pano, tikudziwa kuti anthu 7 mwa 10 aliwonse amagwira ntchito yokhudzana ndi fodya. Tsono kutaya fodya anthu amenewa angadzagwire mtengo wanji,” adatero Kubalasa.

Mkulu wa bungwe loyang’anira za ulimi ndi malonda a fodya la Tobacco Control Commission (TCC) Kaisi Sadala wati dziko la Malawi likuyenera

kuyang’ana za malonda afodya kupyola pa nkhani ya zaumoyo.

Iye wati mokonda dziko lathu, Amalawi sitikuyenera kuvomereza zoletsa malonda a fodya koma kuti tikuyenera kumalingalira za mbeu kapena zochita zina zomwe zingamathandizane ndi fodya pobweretsa chuma msika wafodya ukamatsika.

“Maloto amenewo ngosagwira ku Malawi kuno kunena chilungamo.

Tikuyenera kuyang’ana malonda a fodya pa nkhani ya umoyo inde komanso tiunikirane za chuma cha dziko lathu kuti zikhala motani,” adatero Sadala.

Iye wati cholimbitsa mtima n’choti ngakhale kampeniyi ili mkati, zikuoneka kuti malonda a fodya akuyendako bwino kuyerekeza ndi momwe zidalili m’zaka zingapo zapitazi kusonyeza kuti Malawi ikadali ndi chiyembekezo mu fodya.

Related Articles

Back to top button