Nkhani

Palibe mlendo ku MCP—Munthali

Listen to this article

Pomwe chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chidachititsa msonkhano wake waukulu kumathero a sabata yapitayi mwa mpanimpani pothawa ziletso ku mabwalo a milandu, zidadziwika kuti chipanichi chasintha kayendetsedwe pochoka pokhazikika m’chigawo chapakati nkusefukira mzigawo zonse za dziko lino.

Pamsonkhanowo am’nkhala kale m’chipanichi omwe amachokera m’chigawo chapakati monga Juliana Lunguzi, Max Thyolera, Lewis Chakwantha, Kusamba Dzonzi, Daniel Mlomo, Lyton Dzombe, Jean Sendeza, Rhino Chiphiko ndi ena sadapateko mpando olo umodzi.

Atsogoleri a MCP: Mkandawire, Mia ndi Chakwera

Koma yambiri mwa mipandoyi  idapita kwa ‘alendo’ ochokera ku chipani cha Peoples Party(PP) Sidik Mia, Harry Mkandawire, Cornelius Mwalwanda, Salim Bagus, Ken Zikhale Ng’oma ndi  Catherine Gotani mwa ena.

Izi zikuonetsa kuti maudindo achoka kuchipinda cha MCP komwe n’kuchigawo chapakati ndipo afalikira m’zigawo za kum’mwera ndi kumpoto.

Koma tikayang’ana mmbuyo pa msonkhano omwe chipanichi chidapangitsa m’chaka cha 2013, Lazarus Chakwera yemwe adali mlendo koma wochokera kuchigawo chapakati, adasankhidwa kukhala mtsogoleri pomwe wachiwiri wake adali Richard Msowoya wochokera ku chigawo cha kumpoto ndipo mlembi wamkulu adali Gustave Kaliwo wa kummwera.

Ndipo pamasankho omwe adalipo sabata yathayi, Chakwera adasankhidwa kukhala mtsogoleri wopanda wopikisana naye, pomwe naye Sidik Mia wochokera ku m’mwera adalowa ngati wachiwiri kwa mtsogoleri ndipo Eisenhower Mkaka yemwenso amachokera ku Lilongwe adalowa ngati mlembi wamkulu wachipanicho.

Pomwe mpando wa mneneri udapita kwa mlendo winanso Maurice Munthali yemwe amachokera ku chigawo cha ku mpoto. Mpandowutu udali wa Mkaka, msonkhanowu usadachitike.

Komatu anthu ena izi sizidawakomere ndipo anenetsa kuti chipanichi chidaperekedwa kwa alendo okhaokha maka ochokera ku PP oposa theka kukhala m’mipando ikuluikulu n’kusiya am’nkhala kalewa pofuna kuwasangalatsa.

Koma polankhulapo mneneri wa chipanicho Munthali adati palibe mlendo m’chipani cha MCP chifukwa aliyense adali wa chipanichi ulamuliro wa zipani zambiri usadabwere.

Malinga ndi Munthali, anthuwa angobwerera kuchipani chawo chakale.

Iye adati a mnkhalakalewa akungoyenera kudziwa kuti kayendetsedwe ka ndale kamasintha malinga ndi momwe nyengo ilili.

“Komanso tisaiwale kuti paja mtsogoleri wathu Chakwera, adatsegula khomo kuti aliyense alowe ndipo palibe zoti uyu adali wa PP, kapena Aford kaya DPP ayi,”adalongosola Munthali.

Iye adaonjeranso kuti n’chifukwa cha kutsekulidwa kwa khomoko anthu ambiri akubwera ndipo ngati chipani akufuna anthu ambiri.

“Am’nkhalakalewa asadandaule kapena kuchoka m’chipani chifukwa kubwera kwa anthuku kukungosonyeza kuti chipanichi chili ndi fungo labwino lomwe likuitana anthu,” iye adatero.

Mmodzi mwa akadaulo pa ndale Mustafa Hussein adavomerezana ndi Munthali kuti aliyense adali wa MCP ndipo anthuwa angobwerera ku chipani chawo chakale.

Hussein adati posankha anthu ochokera m’zigawo zosiyanasiyana chipanichi chatenga njira yabwino yoonetsa kuti ndi cha fuko la Malawi osati cha chigawo chapakati chokha.

“Aliyense ali ndi mizu ya MCP chifukwa n’chipani cha kale. Apapa chipani cha MCP chapeza njira yabwino chifukwa ena amati n’cha chigawo chapakati pomwe ena ankati n’cha Achewa. Uku kudali kulakwitsa chifukwa chipanichi sadayambitse ndi Achewa ayi koma achina Orton Chirwa, yemwe adali wa ku Nkhata Bay,” adatero Hussein.

Iye adaonjeranso kuti chipani chiyende bwino ntchito imakhala pomanga maziko osati pa maudindo a kumtundaku.

Related Articles

Back to top button