Malawi ali mumdima wa dzaoneni

Dziko la Malawi laona mdima womwe sudaonekepo chilandirireni ufulu wodziyimira palokha. Madera ena akukhala masiku awiri magetsi osayaka. Kwina, ndiye mpaka kumatha masiku atatu. Akangoyaka, pena sakumatha ola upeza azima kale.

Ophunzira, eni makampani, zipatala, komanso zigayo akubuula mumdima wa ndiweyani. Chipulumutso sakuchiona. Ngakhale zikumveka kuti kukubwera majeneleta, Amalawi akuda nkhawa chifukwa mitengo ya magetsi nawo akuti idzakwera. Mtendere sukudziwika tsiku lomwe ukudza.

 

 

Share This Post