Nkhani

Mavuto a mnanu kwa osamutsidwa

Awa ndi mayi Margaret Julius. Madzi atasefukira m’mudzi mwawo mwa Chililamadzi ku Makhanga m’boma la Nsanje mwezi wa March chaka chatha nthawi ya namondwe wa Freddy, iwo adakwera mu mtengo wa minga. Iwo adakhala mu mtengomo kwa masiku awiri osadya kanthu kufikira pomwe othandiza anthu adadzawapulumutsa pa bwato.

Mayiwa ndi mmodzi mwa anthu a pansi pa mafumu 23 a m’dera la Senior Group Kalonga amene adasamutsidwa kuchoka ku Makhanga kupita m’mudzi mwa Militoni m’bomalo. Boma litalengeza kuti Mankhanga ndi dera limene anthu sayenera kukhalako chifukwa chaka ndi chaka madzi amasefukira kuchokera m’mitsinje ya Ruo ndi Shire, ena adasamukira kwa Militoni pomwe ena adalowera kwa Osiyana.

Malinga ndi mayi Julius, iyi ndi nyumba imene akukhala kuchokera mwezi wa September chaka chatha pomwe adasamukira kwa Militoni, kuchokera pa msasa wa Admarc ku Bangula. ‘Nyumbayo’ ndi pepala la pulasitiki lakuda, nthambi za mitengo ndipo pamwamba mpofolera udzu.

“Ndimagona mmenemu. Ndi chimodzimodzi kugona panja ndithu. Pambali pa malo ogona, vuto lalikulu limene ndikukumana nalo ndi la njala. Sindilotako zobwerera ku Makhanga koma kuno moyo ukuthina,” akutero mayiwo.

Senior Group Kalonga adati mayi Justin adachita tsoka chifukwa sanapeze nawo thandizo la K1 280 000 limene bungwe la GiveDirectly lidapereka kwa lililonse mwa mabanja 966 amene adasamuka ku Makhanga kupita kwa Militoni.

“Nkhani yawo imandikhudza kwambiri. Alibe pokhala pabwino. Kuchoka ku Makhanga adangobwera ndi mabigiri awiri basi. Kochepa kamene timapeza timagawana koma mavuto ndiye aliko,” atero a mfumu Kalonga.

Pocheza ndi anthu ena m’mudzimo, anadandaula kwambiri kusowa kwa chakudya, zipatala, sukulu ngakhalenso madzi abwino. Anthuwo anenetsa kuti alibenso loto lobwerera ku Makhanga koma boma likadachepetsa mavuto amene akukumana nawo.

Mwachitsanzo, mwezi wa August anthu 15 adawatengera ku chipatala atadya mipama kaamba ka njala. Malinga ndi a Kalonga, anthuwo ankangosanza pomwe amawatengera ku chipatala.

Mayi wina a Fanita Bulasha adati akukumana ndi mavuto a mnanu. “Tikadali pa msasa. Mantha akundigwira n’kalingalira kuti mvula iyamba kugwa posachedwa. Mtendere palibe,” atero iwo.

Dandaulo la mayi ena a Sophia Petulo a zaka 62 iwo akudandaula kutalikira kwa chipatala. “Ndimayenera kupita ku chitala cha Phokera kamodzi pa mwezi kukatenga mankhwala a BP. Nthawi zambiri ndimalephera chifukwa pamafunika K7 000 kupita kokha ndiye ndiyipeza kuti?” adazizwa iwo.

Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe la GiveDirectly a Thom Mtenje adati bungwelo lidapereka ndalama zokwana K3.4 biliyoni kwa mabanja 2 700 omwe adakhudzidwa ndi namondwe wa Freddy m’bomalo.

“Tidapereka ndalamazo moduladula katatu ndipo ambiri adagwiritsa ntchito kumangira nyumba, kuyamba bizinesi ngakhalenso kugula ziweto,” iwo adatero.

Malinga ndi nthambi yothandiza pa ngozi zadzidzidzi ya DoDMA, anthu 7 000 adasamutsidwa kuchoka ku Makhanga kupita kwa Osiyana ndi kwa Militoni. Mneneri wa nthambiyo a Chipiriro Khamula ati akudziwa za mavuto amene anthu a msamuko akukumana nawo ndipo akuyesetsa kuwathandiza kupyolera ku khonsolo ya bomalo.

“Tikumvetsa za mavuto amene akukumana nawo, makamakanso pa nkhani ya malo okhala. Timathandiza anthuwa polingalira kuti ndi achikulire, aulumali, omwe ali ndi matenda a mgonagona ngakhalenso ana amene amalerana okhaokha,” atero a Khamula.

Malinga ndi khansala wa wodi ya Mlonda m’bomalo a Cassim Ngwali, mavuto amene alipo ndi ambiri kwaa anthu osamutsidwa kaamba ka madzi osefukira. Koma akuyesetsa kuthana nawo.

“Nkhani ya njala ndi vuto lalikulu. Mwezi wa September tidalandira matumba 20 okha kuti tigaire anthuwa omwe adali ochepa zedi. Kaamba ka kutentha, mijigo 5 imene idaikidwa m’mudzimo siyikutuluka madzi. Mavuto sangathe onse, koma tikuyesayesa,” atero a Ngwali, omwe ndi wapampando wa khonsolo ya boma la Nsanje.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button