Nkhani

MEC yakonzeka kulanga osokoneza

Chisankho cha 2025 chikhoza kuzakhala umboni wa ulamuliro weniweni wa demokalase ngati bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) lizatsate malamulo atsopano.

Malinga ndi mneneri wa bungwelo a Sangwani Mwafulirwa, malamulo atsopanowo azagwiritsidwa ntchito popereka zilango kwa onse osokoneza kapena kuyambitsa ziwawa pa misoonkhano ya kampeni.

Anthu kuvota pa chisankho

“Sitizasekelera aliyense osokoneza chifukwa malamuloa tsopano akutipatsa mphamvu. M’mbuyomu, ndondomeko zimakhazikitsidwa koma padalibe lamulo lotipatsa mphamvu,” anatero a Mwafulirwa

Malamulo atsopanowo akupereka mphamvu ku MEC zopereka chilango cha ndalama zokwana K5 miliyoni.

Malamulowo akuperekanso mphamvu ku MEC zochotsa kandideti yemwe omutsatira apezeka akuyambitsa ziwawa.

“Izi zikutanthauza kuti onse ofuna kudzayimilira m’maudindo osiyanasiyana ayambiletu kuphunzitsa owatsatira zokhudza malamulo atsopanowo chifukwa akhoza kuzawasokoneza.

“Tikhala tikukumana ndi zipani komanso onse okhudzidwa kuti tiunikilane poyenera kusintha. Tikufuna kuti tikamadzafika 2025, zonse zidzakhale zitakonzedwa,” atero a Mwafulirwa.

Pa zisankho zam’mbuyomo, otsatira zipani amachitirana zipongwe n’cholinga chofuna kuopsezana ndi kugwetsana mphwayi ndipo pazipongwe zoterozo, ena adataya miyoyo ndi katundu wawo.

Ngakhale kuti bungwe la MEC limakhala ndi ndondomeko zolondolozera milandu monga yoyambitsa ziwawa kapena kusokoneza kayendetsedwe ka zisankho, a Mwafulirwa ati mchitidwewo umachitikabe.

“Pa zisankho za m’mbuyomu, ndondomeko zimenezi timakhala nazo ndipo wina aliyense opikisana nawo pa chisankho amasainila kuti azikatsata zomwezo pamene akupanga kampeni.

“Vuto linali loti tinalibe mphamvu zolangila amene waphwanya ndondomeko zimenezi. Koma ulendo uno tabwera ndi moto moti onse ozolowera chisokonezo asamale,” Iwo atero.

Mkulu wa bungwe loona kuti andale akutolelana ndi kutsatira ndondomeko za demokalase la Centre for Multiparty Democracy (CMD) a Kizito Tenthani anati malamulo atsopanowo abwera nthawi yabwino.

“N’kale lonse zipani komanso andale amasayina kuti sazapanga mtopola kwa anzawo ndipo azaonesetsa kuti chisankho chikuchitika mwa bata koma chifukwa padalibe malamulo okhwimitsira, zinkavuta,” anatero a Tenthani.

Iwo anati malamulo atsopanowo akunena chindunji zokhudza mchitidwe wonyozana kapena kunyazitsana ndi zilango zake kwa opezeka olakwa pa milandu yotero,  makamaka pano pomwe anthu amatha kunyozana kapena kunyazitsana pa masamba a mchezo.

“MEC itati iikepodi mtima ngati momwe akuneneramo, zikhoza kutichitira ubwino kwambiri. Atati alangeko angapo osokoneza, zisankho zitha kumayenda bwino,” atero a Tenthani.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button