‘Menopause’ ikuwazunguza?
Azakhali,
Zikuonetsa kuti akazi anga atopa nane. Ine ndi akazi anga tonse tili m’zaka za m’ma 30 ndipo tikusiyana ndi zaka 5.
Wamkulu ndine ndipo tili ndi ana atatu. Chikwatirirane, pa moyo wathu wa banja mosabisa zinthu zonse zinali bwino kwambiri. Tikakhala ku ntchito timatha kuyankhulalana pafupipafupi. Ikakhala nkhani ya ku chipinda ndiye panalibe vuto. Zimatha kutheka kuti tonse tili ku ntchito koma kuuzana kuti tikumane malo ena ake ndi kukasewera gemu yathu. Izi zakhala zikuchitika nthawi yonseyi.
Kuyambira chaka chatha akazi anga anasintha kwambiri. Nditawapanikiza kuti andiuze chomwe chikuwavuta anati atopa nane. Akufuna mamuna wina osati ineyo.
Sindinakhumudwe nao chifukwa ndimadziwa kuti akazi amasintha ngati bilimakhwe. Tinatengana kupita kuchipatala kuti akawayeze. Atawayeza zapezeka kuti ali bwinobwino. Ndipo iwo sanayambe kuonetsa zizindikilo zosiya kusiya nsambo, inde menopause m’Chingerezi.
Ndayesa kuwauza kuti tipite m’mapemphero koma akukana. Ine akazi anga ndimawakonda kwambiri ndipo sindifuna kuwazembera.
Akwawo nkhani zonsezi akuzidziwa bwino. Ndipo ayesetsa kukhala nawo pansi koma sakutheka. A ku mpingonso nawo ayesetsa kukhala nafe pansi koma sizikutheka.
Pano akundivutitsa kuti tigawane katundu amene tili naye kuti aliyense ayendere yake. Ukwatiwu ndi wa pa tchalitchi. Mavuto onsewa a ku tchalitchi akuwadziwa ndipo iwo amayankha kuti chilakolako cha ine chinawathera. Ndakhalanso ndikufuna kuti nanga cha mwamuna wina muli nacho? Amayankha kuti ali nacho.
Nditani ine azakhali,
Mwanza.
Zikomo ku Mwanzako,
Ukakhala pabwino, poipa pamakuitana. Mwinatu muli ndi vuto ndi inu? N’kadati mulowere mu Equatorial Guinea akakuthandizeni koma ayi u kasongo winawu wanyanya.
Ngati muli ndi vuto auzeni kuti afotokoze chenicheni ndi cholinga choti mulikonze.
Ngati sizikutheka, asiyeni achite zimene akufuna. Fupa lokakamiza limaswa mphika. Amenewo aponda mwala. Wakhungu akaponda mwala amatha kukugenda nawo mosavuta.
Chikondi ndicho chofunika pa banja ndipo ngati chikondi palibe ndiye kuti banja palibepo.
Anatchereza.