Nkhani

 ‘Mgwirizano ungathetse zipolowe’

Listen to this article

Mgwirizano pakati pa atsogoleri, ngakhale asemphane maganizo pa ndale ndiko kungathetse zipolowe ndi mikangano ya ndale, atero akadaulo.

Iwo adanena izi potsatira chiwembu chofuna kuotcha maofesi a bungwe loona z ku Lilongwe sabata yatha, kuotchedwa kwa galimoto ziwiri za otsatira gulu la United Transformation Movement (UTM) masiku apitawo komanso kuopsezedwa kwa otsatira UTM ku Nyumba ya Malamulo.

Throsell: Zokhumudwitsa

Kadaulo wa zandale ku Chancellor College Mustafa Hussein adatamanda mtsogoleri wa chipani chachikulu cha MCP Lazarus Chakwera komanso mtsogoleri wa UTM Saulos Chilima pogwirana chanza ndi kusekererana ku mwambo wa Angoni Maseko wa Umhlangano. Iye adati izi zimathandiza kuti otsatira zipani zawo aziyanjana, osakhala ndi maganizo a chiwembu kwa amene akutsutsana nawo maganizo.

“Izi nzofunika chifukwa ngati atsogoleri akusonyeza chikondi ndi chimvano chotere, mpovuta kuti anthu otsatira zipani zawo azipanga ziwawa chifukwa aziopa kukhumudwitsa atsogoleriwo,” adatero Hussein.

Kadaulo wina George Phiri wa ku University of Livingstonia (Unilia) adati atsogoleri awiriwa ngofunika kuwayamikira chifukwa chopachika kusiyana kwawo pandale n’kudzichepetsa pamaso pa anthu owatsatira.

“N’zachidziwikire kuti kumwambo umenewo kudali otsatira zipani zonse ndipo adaona zomwe atsogoleri awo adachita. Kotero, anthuwo ngakhale atakhala ndi cholinga cha zipolowe akhonza kusintha maganizo,” adatero Phiri.

Iye adati nthawi idakwana yoti Amalawi azindikire tanthauzo lenileni la ndale za demokalase kuti ndi mpikisano koma ofuna kutukula dziko osati kunyozana kapena kuchitana ziwembi.

“Ndale za demokalase zimafunika kuti zipani zizipikisana pamfundo za chitukuko ndi utsogoleri koma nthawi zambiri timaona otsatira zipani akulimbana ngati kuti simtundu umodzi,” adatero Phiri.

Bungwe la mgwirizano wa maiko la United Nations (UN) lidadzudzula mchitidwe wa zipolowe umene ukupita patsogolo pomwe tikulowera ku chisankho cha pa 21 May 2019.

Mneneri wa UN pa nkhani za ufulu wa anthu Liz Throssell adati zipolowe zimene zakhala zikumvekazi n’zosakoneza.

“Galimoto ya phungu wina Agness Nyalonje idaotchedwa ku Mangochi mmwezi wa August, phungu winaso Patricia Kaliati adakumana ndi mazangazime akufuna kulowa m’Nyumba ya Malamulo mmwezi wa April ndipo atsogoleri amabungwe osiyanasiyana akhala akuwopsezedwa. Izi zikupereka chiopsezo pa demokalase,” adatero Throssell.

Related Articles

Back to top button