Nkhani

Misika ya Admarc siyitsegulidwa msanga

Listen to this article

Nduna ya za malimidwe a Sam Kawale ati kampani yogula mbewu ya Admarc siyitsegulidwa kuti iyambe kugula mbewu pokhapokha anthu oyenera m’mipando ku kampaniyo atapezeka.

A Kawale anena izi potsatira nkhawa za bungwe la alimi la Civil Society Agriculture Network (Cisanet) kuti kuima kwa ntchito za kampaniyo kwapereka danga kwa mavenda lobera alimi.

Misika ya Admarc imathandiza kutsitsa chimanga

Wapampando wa bungwe la Cisanet a Herbert Chagona adatsindika kuti alimi akusowa kokagulitsa mbewu zawo pamtengo wovomerezeka chifukwa msika omwe ukupezeka pafupi ndi wa mavenda.

“Admarc imakomera kuti imapezeka kufupi ndi alimi ndiye chimakhala chowavuta mavenda kubera alimi chifukwa mitengo yawo amapikisana ndi Admarc koma pano atasamo okhaokha m’midzimu,” adatero a Chagona.

Iwo adapempha boma kuti lithamangitse ntchito yokonzanso Admarc kuti kampaniyo iyambe kugula mbewu msanga kuti alimi apezeko phindu ndi mbewu zomwe atsala nazo.

Koma a Kawale ati boma silikufuna kulemba ntchito anthu omwe sangapindulire kampani ya Admarc chifukwa cholinga chotsekela kampaniyo chidali kukonza kagwiridwe kake ka ntchito.

“Anthu asaone kuchedwa chifukwa sitikufuna kulemba ntchito anthu oti sangabweretse kusintha komwe tikufuna. Zonse zikuyenda bwino panopa ndipo tikangomaliza kulemba anthu ofunikira tiyipatsa zofunikira zonse kuti iyambepo,” atero a Kawale.

Iwo ati padakalipano, alimi akhoza kumagulitsa mbewu zawo monga Chimanga kunkhokwe za boma za National Food Reserve Agency (NFRA) komwe boma likugulira chimanga pa mtengo wovomerezeka.

“Tikuyenera kuvomereza kuti Admarc idaonongeka ndipo idalibe tsogolo ndiye zomwe tikupanga pano zikhoza kuoneka ngati zochedwa koma ndi momwe sikuyenera kuchitikira kuti tidzutse Admarc,” atero a Kawale.

Malingana ndi wapampando wa Board ya Admarc a Zachary Kasomekera, kampaniyo ikuyembekezera kulemba ntchito anthu pafupifupi 2 000 ndipo pano idayamba kulemba anthuwo kuyambira mkulu yemwe aziyendetsa kampaniyo a Daniel Baxter Makata.

A Kasomekera adati ina mwa mipando ikuluikulu yofunika kulemberamo akadaulo ndi woyang’anira za chuma, woyang’anira kayendetsedwe ka kampaniyo komanso woyang’anira za ubale wakampaniyo ndi anthu.

Iwo adatsimikizanso kuti ntchito yolemba anthuwo ikadzatha, mpomwe kampaniyo idzayambe kugwira ntchito zake monga momwe zikufunikira.

“Kale Admarc idali ndi ogwira ntchito oposa 3 000 koma tikufuna asapose 2 000 koma akhale anthu oti apititsa patsogolo kampaniyo osati kuibwezera mmbuyo,” adatero a Kasomekera.

Mu September 2022, boma lidatseka kampani ya Admarc kudzera mwa nduna yakale ya za malimidwe a Lobin Lowe litaona kuti kusamvana pakati pa Board ndi akuluakulu akampaniyo kwakula.

Bomalo lidaona kuti kusamvanako kudakolezera kusakaza chuma cha kampani, katangale ndi kuba komanso kuti ntchito za kampaniyo zidalowa pansi kaamba koti polemba ntchito samatsata zoyenereza.

Mu January 2023, Admarc idachotsa ogwira ntchito onse koma mukalata yolengeza izi, kampaniyo idati ilemba mwa kontirakiti ogwira ntchito ena kuti kampaniyo isaimiretu.

Kutsekedwa kwa Admarc kudachititsa kuti mavenda akwenze mitengo ya mbewu monga chimanga kuchoka pa K146 pa kilogalamu m’chaka cha 2021 kufika pa K500 pa kilogalamu.

Related Articles

Back to top button