Msonkhano wa UTM walephereka
Msonkhano womwe komiti yaikulu ya chipani cha UTM imayenera kukhala nawo walephereka.
M l e m b i w a m k u l u wachipanicho a Patricia Kaliyati ati msonkhanowo uchitika mkati mwa sabata ikubwerayi.
A Kaliyati ati malingana ndi zolinga za msonkhanowo, maloya a chipanicho amayenera kukhalapo, koma atangwanika ndi ntchito zina ndiye akuluakulu achipani adagwirizana zosintha tsiku.
“Msonkhano walephereka chifukwa maloya athu akugwira ntchito zina zofunikira ndiye tiwadikira kuti azakhalepo t i k a m a z a k u n a n a n d i kukambirana,” adatero a Kaliyati.
Mneneri wa chipanicho a Felix Njawala adati msonkhanowo ndiwofuna kukambirana za tsiku ndi ndondomeko ya komvenshoni komanso zotuluka m’mgwirizano wa Tonse Alliance.
Iwo adati ganizo lotuluka m’mgwirizanowo lidapangidwa kale ndi akuluakulu a komiti yaikulu nthawi yomwe chipani chinkakhuza maliro a yemwe adali mtsogoleri wachipanicho a Saulos Chilima.
A Chilima adamwalira pangozi ya ndege ya asilikari pa 10 June 2024 limodzi ndi anthu ena asanu ndi atatu pomwe amapita ku maliro a a Ralph Kasambala womwe adali loya komanso adakhalapo mlangizi wa boma pa za malamulo.
Zambiri zidanenedwa zokhudza imfa ya a Chilima ndi anthu enawo zomwe zidapangitsa kuti gulu lina lotsatira chipanicho lizipanga zosemphana ndi mapulogalamu a boma kusiyana atayamba ntchito yawo yokonza za kagwiridwe ka ntchito m’boma nthawi yomwe adali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino.
A Lameck Manda omwe adapuma pantchito ya uphunzitsi ati ntchito yoyendera maofesiyo ndiyofunika kwambiri chifukwa anthu ambiri amavutika akafuna thandizo ku boma.
“Umatha kupita ku ofesi ya boma m’mawa koma umakhala nthawi yaitali eni ake asadafike. Mthawi zina mpaka ndiye umangobwelera n’kuchita kudzapitanso. Choncho akamawagwededza, akhoza kusintha,” atero a Manda.
Koma a Mangulama adati pomwe boma likugwedeza ogwira ntchito, liziwonetsetsa kuti zipangizo zogwilira ntchitoyo zikupezeka mosavuta komanso ogwira ntchitowo akusamaliridwa.
Boma la Tonse Alliance litangolowa, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera adalonjeza kuti boma lawo lisintha momwe anthu amagwilira ntchito m’boma kaamba koti zambiri zidali zitawonongeka.
A Usi adasankhidwa kukhala wachiwiri kwa Pulezidenti mwezi wa Juni 2024 kutsatira infa ya a Chilima.n
ankapangira. ndi momwe a Chilima
A Chilima amapezeka m’mapulogalamu onse aboma, koma akuluakulu omwe aku y e n d e t s a chipanicho sadapezeke kolumbiritsa a Michael Usi omwe adalowa m’malo mwa a Chilima ngati wachiwiri kwa Pulezidenti wa dziko lino.
Kupatula apo, atsogoleri a chipanicho adakonza mwambo wokakumbukira a Chilima ku Nkhalango y a C h i kangawa pa t s i ku l omwe boma limapanga mwambo wina wokumbukira a Chilimawo ndi anthu ena.
A ku l u a ku l u e n a m’chipanicho adapempha mamembala ena omwe akugwira ntchito ndi boma monga nduna zaboma kuti atule pansi maudindo, koma ena monga nduna ya zokopa alendo a Vera Kamtukule adakana kuchoka m’boma.
“Sindingatule pansi u d i n d o c h i f u k w a ndidasankhidwa kuti ndizatumikile Amalawi,” adatero a Kamtukule.
Mgwirizano wa Tonse Alliance udayamba mchaka cha 2020 pokonzekera chisankho cha Pulezidenti chachibwereza khothi l i t a t h e t s a z o t s a t i r a za chisankho cha 2019 chomwe a Peter Mutharika woyimira chipani cha DPP adapambana.
Nkhawa yaikulu pa nthawiyo idali chinsinsi chomwe chidalipo pa mgwirizanowo ngakhale kuti mkatikati mwa ndime zidutswa zake zidayamba kutulukira poyera.
Omwe ankadziwa zinsinsi za mgwirizanowo adali a Chilima ndi a pulezidenti a Lazarus Chakwera ndipo akadaulo pa ndale adachenjeza ku t i c h i n s i n s i c h o chikhoza kudzabweretsa chisokonezo patsogolo.
Cholinga chenicheni cha mgwirizanowo chidali kuchotsa a Mutharika ndi chipani cha DPP m’boma potsatira zionetsero zotsutsa ulamuliro wa DPP zomwe Amalawi dziko lonse ankapanga chitatha chisankho cha 2019.