Mugwiliranji bere la mwini?
Masiku apitawa mtsikana wina adandifotokozera za momwe mphongo ina idagwirira bere lake pa msewu mumzinda wa Lilongwe.
Mtsikanayu adali akungodziyendera mutauniyo pomwe adangodzidzimuka mkono wa bambo yemwe amabwera kutsogolo kwake uli pabere lake.
Mmene amati azilankhula, bamboyo nkuti atayamba kuyenda kupitiriza ulendo wake ngati sadachite kalikonse.
Mtsikanayo adangoti kakasi, kenaka adangopitiriza ulendo wake ali cheucheu kuti bambo wina asamuonererenso.
Nkhaniyi idandikumbutsa zomwe zidandionekera mutauni ya Limbe, ku Blantyre, zaka zinayi kapena zisanu zapitazo.
Anthu adali pilingupilingu m’mawa wa Loweruka limenelo ndipo ndidali pandawala kukwakwera basi pomwe ndidangozindikira mkono wa mnyamata wina, yemwe ndidali ndisadamuoneko chibadwire, uli pabere langa.
Ndikudzidzimuka, mnyamatayo, yemwe timayenda mosemphana, adapitirira ulendo wake akumwetulira ngati sadachite chilichonse chodabwitsa.
Ndidangoti kakasi, kusowa cholankhula mnyamatayo akulowelera m’gulu la anthu omwe anali akuyenda pamalopo.
Amayi ndi atsikana omwe zangati izi zidawaonekerapo angachitire umboni za mkwiyo ndi manyazi omwe amadza zoterezi zikakuchitikira, poti ena zawachitikira m’maofesi, kusukulu ndi malo ena.
Kwa nthawi yaitali ndidakhala ndikudzifunsa za mmene ndikadakhaulitsira ndoda yachipongweyo.
Ndikadakuwa? Koma ndi changu chimene mnyamatayu adachita, ndimakaika ngati ena omwe amadutsa pamalopo adaona zomwe zidachitika. Akadandikhulipilira ndani? Umboni sukadavuta kodi?
Kapena ndikadamumenya? Koma mwachidziwikire akadabwenzera ndipo mwinanso nkadavulazidwa ndine ndemwe.
Ena nkumati atsikana mukumadziitanira mavuto nokha kaamba kamavalidwe kosadzilemekeza, koma ichi sichifukwa chokwanira mpang’ono pomwe choti anthu ena azichita zomwe afuna ndi matupi a amayi.
Kaya wina atavala zoonetsa mawere ake, palibe choyenereza bambo kapena mnyamata kugwira mawerewo. Tisaiwale kuti m’dziko muno muli ufulu wa kavalidwe.
Kwa amayi, ndikukhulupilira kuti kungopenya ngati momwe ndidachitira ine ndi msungwana wa ku Lilongweyu, sikungathandize kwenikweni.
Ngati pali chomwe mungathe kuchita kuti abambo oterewa aonekere poyera, chitani, kuti aone polekera.