Mukufuna kulima chamba?
Kwa nthawi yaitali, chamba chakhala chikulimidwa m’dziko muno mozembera malamulo. Komatu makono kwadza chamba chosazunguza bongo chimene akuchitama kuti chikhonza kutembenuza chuma cha dziko lino. Komatu ofuna kulima chamba cha mafakitalechi akonzeke kutulutsa kaye K7.6 miliyoni kuti apeze layisensi.
Unduna wa zamalimidwe wati makampani ndi magulu aalimi omwe akonzeka ndipo adula chiphaso cholimira mbewu ya chamba akhoza kuyamba kulima chaka chino.
Koma mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Frighton Njolomole wati K7.6 miliyoni n’chiletso kuti alimi aang’ono asachite nawo ulimiwu.
Iye adati alimiwo azingolionera phindulo likudutsa umooo! “N’zokomera makampani ndi makopaletivi okhazikika bwino chifukwa ndalamazo zizidutsa K7.6 miliyoni akaphatikiza zofunika zonse kuti alime n’kufika pogulitsa. Si ntchito ya masewera pakufunika mpamba,” watero Njolomole.
Nduna ya zamalimidwe Lobin Lowe idalengeza pa 20 November 2020 kuti nthambi yoyendetsa ulimiwu itaunika bwino idaona kuti chiphaso cholimira chamba chikhale K7.6 miliyoni ($10 000).
Koma malingana ndi ndondomeko za nthambi yoyendetsa ulimiwo, chiphaso chiziperekedwa kwa makampani ndi makopaletivi okhazikika okhaokha.
“Tizifuna umboni woti ndi kampani kapena kopaletivi yodziwika, ali ndi mpamba wokwanira, ali ndi malo okwanira komanso apeza kale msika,” ikutero ndondomekoyo.
Mneneri waunduna wa zamalimidwe Gracian Lungu wati undunawo udavonereza kale zoti ulimiwo uyambe chifukwa kafukufuku wake adatha ndipo ubwino wa mbewuyo udapezeka.
“Ubwino waulimiwu ndi woti boma lizipezapo msonkho, alimi azipha makwacha, anthu apeza ntchito mminda ndi mmakampani okhudza za chamba,” watero Lungu.
Iye watinso pali ndondomeko zomwe zakhazikitsidwa kuti anthu asapezelepo danga lolima chamba chozunguza bongo pobisalira m’chamba chovomerezekachi.
Ndipo alimi eni ake ati boma likadaganizira zokhwefula ndondomeko ya zofunika paulimiwo kuti nawonso apindule nawo paulimiwo.
“Akadakhwefula mtengo kuti nafe tizilima n’kumagulitsa ku makampani omwe azikagulitsa kunja ngati momwe momwe timapachitira ndi bale, kampopi ndi chikopa,” adatero Maliko Dziyende mlimi wa fodya kwa Nkhwazi ku Mchinji.
Wolakhulapo pa zochitika m’dziko Stanley Onjezani Kenani adaikira kumbuyo alimi kuti mtengo wachiphaso omwe boma lakhazikitsa n’chiletso kwa iwo.
“Nkhani ya ulimiwu ndi yabwino koma zomwe boma lapanga pamtengo wachiphaso zili ngati kupereka ndi dzanja ili n’kulandanso ndi dzanja linali chifukwa apapa alimi ang’onoang’ono palibe chawo,” adatero Kenani.
Malingana ndi unduna wazamalimidwe, makampani ndi makopaletivi oposa 100 adapereka kale kalata zokhumba kuchita nawo ulimiwu ndipo nthambi yoyendetsa ulimiwo ikuwaunika.
Lamulo lovomereza ulimi wa chamba lidakhazikitsidwa mdziko muno mmwezi wa February 2020 ndipo lidasainidwa ndi Pulezidenti Peter Muntharika (mu May 2020 yomweyo.
Nthambi ya zakafukufuku waulimi ya Chitedze Research Station idafufuza mbewuyi ulendo mvula zitatu nkuvomereza kuti ndiulimi wotheka komanso wofunika ku Malawi.