Nkhani

Ng’anga zaithina itakanika kudzutsa munthu wakufa

Ng’anga ina ku Balaka yapereka chindapusa cha K90 000 kupewa kukaseweza miyezi 15 imene adamugamula atapezeka wolakwa pa mlandu woti adanamiza anthu kuti adzutsa mwana wakufa.

Ng’angayo, Frazer Satha wa zaka 37 wa m’boma la Ntcheu wapereka chindapusacho pa wobera munthu pomunamiza.

Mneneri wa apolisi m’boma la Balaka a Gladson M’bumpha ati izi zidachitika pa khoti la majisiteleti m’boma la Balaka komwe ng’angayo idaitanidwa kuti ikagwire ntchito yomwe idalepherayo.

“Ng’angayo yapereka chindapusa chifukwa idapatsidwa mwayi wosankha pakati pokaseweza zaka 15 ku ndende kapena kupereka chindapusacho moti pano yapita kwawo,” adatero a M’bumpha.

Woimirira boma pa milandu m’boma la Balaka a Sub-Inspector Mercy Chande adauza khotilo kuti a Satha adatenga K45 000 kwa a Yamikani Tobias powauza kuti adzutsa mwana wawo yemwe adamwalira.

Chifundo wa zaka 18 yemwe adali mwana wa a Tobias adamwalira mu August 2022 atagwera pa chitsime ndipo makolo ndi abale ake adaika malirowo.

Koma a Chande adauza khoti kuti ataika malirowo, mlamu wa a Tobias adakatenga a Satha kuchoka ku Ntcheu kuti adzadzutse malemuyo koma amafuna chipondamthengo cha K45 000.

“Ng’angayo imayenera kugwira ntchitoyo m’dera la Andiamo pa mchombo pa boma la Balaka. Iyo idatsimikiza kuti ikwanitsa kudzutsa malemuyo ndipo idalandiradi K45 000 koma idalephera kudzutsa wakufayo,” adatero a Chande.

Poona kuti ndalama zapita koma palibe chizindikiro choti malemuyo adzuka, a Tobias adakamang’ala ku khoti komwe a Satha adawatsegulira mlandu wobera munthu pomunamiza.

A Satha adakana mlandu wa kuba koma adavomera wonamiza munthu ndipo adawapeza wolakwa popanga zosemphana ndi gawo 319 ya malamulo koma iwo adapempha kuti khoti liwapatse chilango chopepuka chifukwa ali ndi banja lomwe limadalira iwowo.

Koma a Chande adapempha khoti kuti lipereke chilango chokhwima kuti anthu ena a maganizo ndi mtima ngati wa a Satha atengerepo phunziro kuti mchitidwewo uthe.

Woweruza mayi Lucy Mukawa adagwirizana ndi a Chande ndipo adagamula kuti a Satha alipire chindapusa cha K90 000 kapena apo ayi akaseweze zaka 15 ku ndende.

Anthu ambiri odzichemerera kuti ndi ng’anga m’dziko muno amadzinenerera kuti ali ndi mankhwala othana ndi mavuto osiyanasiyana kuphatikizapo nthenda za mgonagona.

Ena mwa anthu otere amakakamiza amayi kugonana nawo powauza kuti akatero awatsegula njira yachibelekelo ndipo alandira mphatso ya mwana ngati ali osabereka.

Enanso mwa anthu oterewa amabera anthu powanamiza kuti iwo amachulukitsa ndalama koma mapeto ake amawabera ndalama zomwe Iwo amapereka kuti awachulukitsirezo.

Pofuna kuthana ndi vutolo, nthambi yoona za mankhwala mogwirizana ndi nthambi yowona za zoulutsa mawu ndi kufalitsa nkhani ya Macra adaika lamulo loletsa kugwiritsa ntchito mankhwala achikuda pokhapokha nthambi yoona za mankhwala itavomereza.

A Satha amachokera mmudzi mwa Madzenje kwa mfumu yaikulu Kwataine m’boma la Ntcheu.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button