Nkhani

NRB ilembere opanda ma ID

Pamene kalembera wa amene akufuna kudzavota pa Chisankho Chachikulu cha pa 16 September chaka cha mawa ali mkati, anthu amene akadasemphana ndi kalemberayo kaamba kosowa chitupa cha unzika (ID) akhoza kumwemwetera pomwe bwalo la milandu dzulo lagamula kuti nthambi yoona za unzika ya NRB iyenera kupezeka malo onse ovotera ndi kulembetsa amene alibe ma ID.

Gawo loyamba la kaundulayu l i d a y a m b a L o l e m b a m’makhonsolo 14 m’dziko lino amene akukhudza madera a phungu 75 ndi makhansala 161 m’dziko lino. Bungwe la zisankho la MEC limabweza anthu amene maina awo sanapezeke m’kaundula wa nthambi yoona zolembetsa unzika ya NRB.

Bungwe la MEC idakhazikika pa Gawo 2 (12) la malamulo oyendetsera zisankho lomwe l i m a t i m u n t h u a k h o z a kulembetsa m’kaundula wa zisankho pogwiritsa ntchito chiphaso cha unzika ngati umboni woti ndi nzika ya Malawi komanso adaf ika msinkhu woponya voti.

Koma Amalawi okhudzidwa 5 kuphatikizapo chipani chotsutsa cha Democratic Progressive (DPP) adapita ku khoti kukasuma kuti achotse lamulo lovomereza anthu okhawo amene adalembetsapo za chiphaso cha unzika (ID) kuti ndiwo awalole m’kaundula wa kalembera wa Chisankho Chachikulu.

A George Chipwaila, Geoffrey Banda, Alex Phillip Dimba, James Chitsulo, and Crino Masulani adafuna bwalo ku t i liletse zoti chitupa cha unzika chikhale chitupa chokhacho chimene anthu angagwiritse ntchito polembetsa.

Popereka chigamulocho d z u l o a M a n d a l a Mambulasa anati: “Pofuna kuti ufulu wa anthu osaphwanyidwe komanso podikira kuti bwalo lina lidzagamule ngati lamulo la chisankho likuphwanya ufulu wa anthu, a NRB apezeke mmalo onse ndi kulembetsa anthu amene sanalowe m’kaundula wawo.”

Woimira MEC pa mlanduwo a David Matumika Banda adati iwo akadakhala odabwa bwalolo likadamvera z i m e n e a m a n e n a okamang’alawo kuti kalembera wa zisankho aime kaye.

“Tikhala limodzi ndi a NRB kuti zomwe anena a bwalo zitheke,” adatero iwo.

NRB ili ka l e n d i maofesala mmalo omwe kaundulayu akuchitika.

Ndipo yemwe amaimira anthu asanuwo a Felix Tambulasu adati iwo saitengeranso nkhaniyi kwina chifukwa anthuwo akalembetsa mavoti.

“Bwalo lati anthuwo akhoza kukalembetsa chifukwa a NRB ndi a MEC azigwirira ntchito limodzi,” atero iwo.

Mmbuyomu, mkulu wa bungwe l o ma y i Annabel Mtalimanja adati anthu amadandaula chifukwa bungwelo lapanga ndondomeko ndi bungwe lopanga za unzika kuti azigwirira ntchito limodzi.

“Amene alibe chiphaso koma akudzimva kuti ndiwololedwa kuvota, adzangonyamuka n’kupita kokalembetsa. Kumeneko akapeza gome la NRB akal embetsa kenako nkupita pa gome la MEC nkulembetsa,” adatero a Mtalimanja.

Koma mmbuyomo, bungwe la a za malamulo la Malawi Law Society ( M L S ) k o m a n s o nthambi yoonetsetsa kuti ufulu wa Amalawi siukuphwanyidwa la Malawi Human Rights Commission adaunikira kuti lamuloli si labwino n d i p o l i m a f u n i k a okhudzidwa nzisankho amang’ale msanga nthawi isadathe.

Bungwelo lidati gawo 77 ya malamulo a pamwamba a dziko lino, constitution m ’ C h i n g e r e z i , limapereka mpata kwa M m a l a w i a l i y e n s e yemwe adafika zaka 18 kuponya voti popanda chomulepheretsa.

“Malamulo amati ndime i l i y o n s e y a malamulo yotsutsana ndi lamulo lalikulu la dziko silikhala ndi mphamvu n ’ c h i f u k w a c h a k e tidaunikira mmbuyo muja tidaunikira kuti ofuna akamang’ale msanga,” adatero Pulezidenti wa MLS a Patrick Mpaka.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button