Nkhani

Ntchito yomanga njanji iima

Listen to this article

Ntchito yomanga njanji yochoka ku Kachaso kupita ku Nkaya ayiimitsa mpaka kampani ya  Mota-Engel ndi ogwira ntchito kukampaniyo atamvana chimodzi.

Ogwira ntchitowo akunyanyala pofuna kukakamiza mabwana awo kuti awakwezere malipiro komanso kuti nzika 300 za ku Thailand zipakire.

Kunyanyalaku kudayambira Lolemba pa 24 June ndipo Lachiwiri Nduna ya za Ntchito Eunice Makangala idatsetserekera kumeneko kukalankhula ndi ogwira ntchitowa kuti abwerere kuntchito koma izi sizidaphule kanthu chifukwa pofika Lachitatu mmawa n’kuti ogwira ntchitowa asadabwerere kuntchito.

Mmodzi mwa ogwira ntchito kumeneko ndipo akuchita nawo sitalakayo koma sadafune kutchulidwa dzina  adauza Tamvani Lachitatu kuti iwo sagwira ntchito mpaka dandaulo lawo litamveka.

“Ndikukamba pano anzathu akubwera kuchokera ku Mwanza kudzatithandiza sitalakayi, sitibwerera kuntchito mpaka titaona malipiro athu akukwera komanso anthu omwe achoka m’dziko la Thailand akubwerera kwawo,” adatero mkuluyo.

Padakhota nyani mchira mpakuti kampaniyi sabata zitatu zapita akuti inathotha gulu la ogwira ntchito kumeneko omwe ndi a m’dziko muno ndi kulemba ena ochokera ku Thailand.

Anthuwa akuti ndi pafupifupi 300 koma chenicheni chomwe amabwerera m’dziko muno sichioneka chifukwa ena sadziwa ntchito ndipo amachita kuphunzitsidwa ndi Amalawi.

Chodabwitsa n’chakuti  malipiro a akunjawo  adali okwera kuposa a Amalawi omwe amatha ntchito.

“Ntchito yake yomwe akugwira ndi kuyendetsa mathirakitala ndi a mabewula zomwe Amalawi timatha, ena mwa alendowo sakuthanso kugwira ntchito ndipo tikuwaphunzitsa ndife. Tikudabwa kuti izi zikuchitika bwanji? Nanga n’chifukwa chiyani akulandira ndalama zoposa ife omwe tikutha ntchito?” adadabwa mkuluyo.

Malinga ndi iye, Amalawi akulandira ndalama yosaposa K30 000 pomwe akamuna akunjawa akumatula makwacha owaposa iwo.

Koma Makangala adati walankhula ndi akuluakulu a kampaniyi kuti mamulumuzana a m’dziko la Thailand omwe alibe ukadaulo wa ntchito apakire ndipo azipita.

Lolemba, mkulu wa kampaniyi Jose Denis da Silva wati akuluakulu a kampaniyi akukambiranabe ndi ogwira ntchitowa ndipo iye adapereka chiyembekezo kuti kusamvanaku kutha popanda zovuta.

Mota-Engel ndi kampani yomwe yalemba kampani ya ku Brazil yotchedwa Vale kuti imange njanjiyi yomwe ikuchokera ku Moatize ku Tete mpaka ku Nacala Port m’dziko la Mozambique kudutsira m’dziko la Malawi.

Malinga ndi yemwe amatitsina khuku pankhaniyi, pofika Lachinayi akuti mbali ziwirizi zinalepherabe kugwirizana ndipo zomwe auzana n’kuti zokambirana zidzachitike Lachiwiri sabata ikudzayi.

“Izi zikusonyeza kuti sitigwira ntchito mpaka Lachiwiri lomwe tidzagwirizane mfundo zenizeni tisanabwerere ku ntchito. Pazokambiranazo akutinso kubwera akuluakulu ena a kampaniyi ochokera m’mayiko ena komanso mbali ya boma.

“Sitikusinthika pa mfundo zathu kuti akuluakulu a dziko la Thailand azipita ndipo timva kuti pomwe tikumane Lachiwiriro atiuza zotani,” adatero mkuluyo.

Pomwe timalemba nkhaniyi n’kuti yankho pa kunyanyalako lisanadziwike.

Kampani ya Mota idalemba Amalawi oposa 3 000 omwe akugwira ntchito zosiyanasiyana kumeneko.

Related Articles

Back to top button