Nkhani

Okalamba 46 aphedwa zaufiti

Anthu okalamba 36 adaphedwa pakati pa January ndi December 2019 pomwe ena 10 adaphedwa pakati pa January ndi September 2020 m’madera osiyanasiyana m’dziko muno powaganizira kuti amachita zaufiti.

Izi zikuchitika pomwe malamulo a dziko  lino a 1911 amakana zoti kunjaku kuli ufiti ndipo gawo 4 la lamulolo limati munthu wonena mnzake kuti ndi mfiti waphwanya malamulo pomwe gawo 6 limati munthu wodzithemba kuti ndi mfiti, ameneyonso waphwanya lamulo chifukwa choyerekeza ufiti.

Kadadzera: Osalanga nokha owaganizira

Malingana ndi lipoti la bungwe la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), ambiri  mwa anthuwa ndi a zaka zoposa 65 ndipo lipotilo likuti ambiriwo amawaganizira ufiti chifukwa cha maonekedwe awo.

Ngakhale zili choncho, m’dziko muno  muli ndondomeko yotetezera anthu okalamba ku nkhanza zosiyanasiyana zomwe anthu ena angakonze kuti awachitire potengera kufooka kwawo kaamba kaukalambawo.

“Kudzera mundondomekoyi, boma limafuna kukwaniritsa chilinga chake choteteza anthu okalamba makamaka poonetsetsa kuti  akulandira maufulu awo moyenera ngati munthu aliyense. Imafunanso kuonetsetsa kuti anthu okalamba akudzidalira, akulemekezedwa komanso sakuchitiridwa nkhanza ya mtundu uliwonse,” ikutero ndondomekoyo.

Lipoti la CHRR likusonyeza kuti ambiri mwa anthu okalambawo amaphedwa potsatira mphekesera chabe kuti amachita zaufiti makamaka m’dera lawo  mukagwa maliro kapena matenda okayikitsa.

Mkulu wa bungwe la CHRR Michael Kaiyatsa wati boma likuyenera kunjenjemera ndi chiwerengero cha nkhalamba zomwe zikuzunzidwa poganiziridwa  ufiti ndipo lichitepo kanthu.

“Tikunena pano, chiyembekezo chonse cha anthu okalamba chili mmanja mwa boma chifukwa zikuwoneka kuti ngakhale ophunzitsa akuyesetsa, anthu sakusintha khalidwe moti boma likapanda kuchitapo kanthu, anthuwa azizunzidwabe,” adatero Kaiyatsa.

Polingalira za nkhanza zomwe anthu okalamba amakumana nazo pa nkhani zokhudza ufitizo, boma kudzera ku unduna wazamalamulo lidayamba ndondokemo younikanso lamulo lokhudza zaufuiti mchaka cha 2006.

Gulu limodzi lomwe limagwira nawo ntchitoyo ndi la anthu omwe sakhulupilira zoti kunja kuli ufiti ndipo yemwe adali mkulu wa gululo pa nthawiyo George Thindwa adati gululo lidangokwanitsa kuyenda kummwera ndi pakati koma silidakafike ku mpoto.

“Pano sindikudziwa kuti zili pati komanso ndidazisiya chifukwa ndidaona kuti anthu sakumvetsetsa za nkhani imeneyi. Nzongomvetsa chisoni kuti anthu amasankha kuchitirana nkhanza pazinthu zopanda umboni,” adatero Thindwa.

Mneneri wapolisi James Kadadzera adati nkhani zokhudza ufiti zakhaladi zikuchitika kwa nthawi yaitali ndipo apolisi mothandizana ndi magulu ena akhala akuyenda m’madera kuphunzitsa anthu za lamulo lokhudza ufiti.

“Kunena zoona mbali yathu timapanga ndipo palibe dera lomwe anthu anganame kuti sadamveko za lamulo lokhudza ufiti,” adatero Kadadzera.

Related Articles

Back to top button