Nkhani

Red Cross igawa magombeza 6, 720

Listen to this article

 

Bungwe la zachifundo la Malawi Red Cross Society (MRCS) layambapo ntchito yogawira Amalawi ovutika, ana amasiye ndi okalambam’maboma 14 a m’dziko muno.

Ntchitoyi idayamba sabata yatha m’boma la Mangochi komwe anthu 480 adalandira zofundazi, zomwe zidachokera kubungwe lina lotchedwa Japanese Blankets for Africa Campaign la ku Japan ndipo zadya ndalama zokwana K40 miliyoni.Flood_camp_in_nsanje

Wachiwiri kwa wamkulu wa bungweli, Lizzie Mwambazi, aduza Tamvani kuti chaka chilichonse bungweli limagawa magombezawa nyengo yozizira ikafika pofuna kuthandiza anthu ovutika.

“Takwanitsa zaka 20 tsopano tikugwira ntchito imeneyi ndipo tagawapo magombeza okwana 250 000 kwa ana amasiye, anthu okalamba ndi ovutikitsitsa. Chaka chino talandira magombeza 6 720 omwe tigawe m’maboma 14, kutanthauza kuti boma lililonse anthu 480 ndiwo achite mwayi,” adatero Mwambazi.

Iye adati bungwe lawo limapereka thandizo losiyanasiyana kwa anthu potengera nyengo ndi zomwe zikusowa kwambiri panthawiyo ndipo adaona kuti nyengo yozizira anthu ambiri ovutika amakongwa.

Woyendetsa ntchito za kuofesi ya DC m’boma la Mangochi, Bissaih Mtayamanja, adapempha anthu omwe adalandira nawo magombezawo kuti asagulitse koma akagwiritse ntchito yake podzitchinjiriza kumphepo.

Iye adapempha anthu omwe sadalandire nawo magombezawo kuti asadandaule chifukwa thandizo ngati limeneli lochokera kumabungwe limafika pang’onopang’ono kuti anthunso azilandira pang’onopang’ono.

“Tikudziwa kuti anthu ofunika kulandira thandizo ngati limeneli alipo ambiri koma ochepa okha ndiwo achite mwayi lero ndipo kukadzabwera thandizo lina, enanso adzalandirako, choncho osachitirana nkhanza kapena nsanje, ayi,” adatero Mtayamanja.

Iye adapemphanso anthu akufuna kwabwino omwe ali ndi kangachepe kuti atengerepo mtima womwe amaonetsa anthu a ku Japan poperekako kangachepeko kuti anzawo ovutika azipezako thandizo.

Gulupu Mapira, yemwe mwambo wogawa magombezawo udachitikira m’dera lake, adati nzomvetsa chisoni kuti mabungwe akufuna kwabwino akamabwera ndi thandizo, anthu omwe amapatsidwa udindo wosankha anthu kapena kugawa amachita chinyengo.

Iye adapempha anthu m’maboma ena momwe katunduyu akupita kuti aonetsetse kuti anthu ovutika zenizeni ndiwo akulembedwa pamndandanda wa anthu olandira nawo, osati abale kapena anzawo.

“Kulandira thandizo ngati ili sikoyamba koma zimadandaulitsa kuti anthu omwe amayeneradi kulandira nawo akubwerera kwawo manja ali m’khosi ndipo mchitidwe umenewu umachitika ngakhale pogawa chakudya kapena zipangizo zaulimi ndi ziwiya za m’nyumba kwa anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi,” adatero Mapira.

Iye adapempha mwapadera kuti mabungwe asaiwale kukhazikitsa ntchito yogawa chakudya chifukwa madera ambiri anthu sakolola mokwanira kaamba ka momwe mvula idagwera chaka chino.

Related Articles

Back to top button