‘Si ife oyendayenda’
Amayi amene ali ndi mwana kapena ana koma si ali pa banja si mahule, momwe ena amaganizira, watero mlembi komanso mkonzi wa mabuku a Wonderful Mkutche.
A Mkutche, omwe alembapo mabuku a oimba otchuka monga Lucius Banda, adanena izi Loweruka ku mwambo wokhazikitsa buku la yemwe adayambitsa bungwe la amayiwa la Single Mothers Empowerment Organisation, Venia Bakali.

Mwambo wokazikitsa buku la Solo with a Purpose udachitikira ku Amaryllis Hotel mu mzinda wa Blantyre ndipo a Mkutche adati bukulo ndi labwino kwa amayi otere popeza likufotokoza momwe angakhalire moyo wa chimwemwe pakati pa mikwingwirima kuphatikizapo chitonzo.
“Amayi omwe ali ndi ana koma siali pa banja amaweruzidwa ndi dziko ngati mahule kapena omwe akhonza kukangalika kulanda amuna aeni ake zomwe si zili chomwecho,” adatero iwo.
A Mkutche adaonjeza kuti amayi akawerenga bukulo akhala odzidalira, opanda nkhawa komanso azidziona kuti siokanidwa koma nawonso ndi wofunikira kwambiri.
M’mawu ake, Bakali adati pa mkumanowo amafunanso kugawana ndi amayiwo ndi kuwalimbikitsa kuti sali wokha.
“Timayenera kulimbikitsana ndi kuunikirana momwe tingakhalire wodzidalira ndi kuchotsa moyo wodzimva kuti ndife osafunikira. N’chapamwamba kuti pastikuli ndakhazikitsa buku lomwe ndalemba lotchedwa kuti Solo with a Purpose m’Chingerezi,” adatero iwo.
Bukulo likufotokoza za moyo wawo ndipo likulimbikitsa amayiwo kuti azidzikhulupirira.
Mmodzi mwa amayiwa a Martha Lisa Wataya omwe amachita bizinesi monga ya shopu yogulitsa za ana, malo odyera ndi kupereka katundu ku malo osiyanasiyana adati mu mzindawu adati udali msonkhano wa phindu omwe walimbikitsa amayiwo kuchilimika n’kumadzidalira pa chuma.
Alinafe Kanjanani, yemwe ndi chiphadzuwa cha chikhalidwe adati waphunzira zambiri monga momwe amayiwa angalumikizanire ndi ana ake komanso momwe angapezere zofuna zawo.
“Nthawi zambiri timachilimika kusaka ntchito zomwe tidaphunzira kuiwala ana athu omwe amakhudzidwa chifukwa amakhala ndi zosowa zawo. Zidali bwino kuti tinakumbutsana momwe tingapoletsere mabala osapeweka m’mabanjamu,” adatero Kananji.



