Thandizo sakakamiza, watero Namadingo
Pomwe chiyembekezo cha mafumu cha anthu a ku Mangochi chili mmwamba kuti maambulansi amene adafa ndipo woimba Patience Namadingo anadzipereka kuti akhoza kuwakonza, zinthu zingatembenuke chifukwa woimbayu wati akhoza kusintha maganizo n’kukadzutsa galimotozi m’madera ena.
Nkhani yake mwina n’kufanana ndi imodzi mwa nyimbo zake yotchedwa Chikondi Sakakamiza chifukwaa iyeyu akuti: Thandizo sakakamiza.

Lachiwiri lapitali, DC wa boma la Mangochi adauza Namadingo kuti akalembe kaye kalata ngati akufuna kukonza maambulansi amene adali mbweee m’masamba a mchezo.
Atakambirana m’kachipinda komata pafupifupi maola anayi omwe anali nawo ndi DC wa boma la Mangochi a Davie Chigwenembe, komanso akuluakulu ena a khonsoloyi, namatetule pa maimbidweyu adamuuza kuti atsatire dongosolo polemba kalata ya zomwe akufuna kuchita.
“Ngati khonsolo tayamba kale kukonza galimoto zisanu mwa galimoto 9. Koma timpatsa zotsalazo pokhapokha akatsatira ndondomeko zoyenera monga kutilembera kalata,” adatero a Chigwenembe.
Koma Namadingo adati: “Zikuoneka kuti a ku Mangochi sadaziyendetse bwino. Tidakumana ndi a DC ngakhalenso woyendetsa za umoyo kuti tikamve momwe zimakhalira. Adatiuza kuti tilembe kalata kuti aone ngati n’koyenera kuti atilole kapena ayi. Apa tidangoona kuti mwina sakufuna. Tiwalemberabe koma thandizo sakakamiza.”
Nkhani ya mtsutso pa zokonza galimoto za mtundu wa Toyota Land Cruiser imeneyi yakhudza anthu a m’bomalo..
Mayi Janet Hassan wochokera m’dera la mfumu Chimwala ati khonsolo ya Mangochi idayenera yayamba yaunikira kukula kwa vuto la mayendedwe isadaimitse Namadingo kukonza galimotozo.
“Amayi oyembekezera ochuluka ku Mangochi akumachilira pa msewu asadafike ku chipatala kaamba ka mavuto a mayendedwe ndiye nkhani yokonza ambulansi si yokambilanamso ayi. Amulore Namadingo akonze galimotozi,” anatero a Hassan.
Mfumu Mapira ya m’bomalo idayamikira ganizo la Namadingo lofuna kukonza maambulasiwa koma adalimbikitsa katswiriyo kutsata ndondomeko zoyenera monga mmene khonsolo ya Mangochi yamulangizira.
Iwo atsindika kufunika kotsata ndondomeko zoyenera pofuna kufikira ndi thandizo losiyanasiyana ofesi za boma.
Katswiri pa nkhani za umoyo yemwenso ndi mkulu wa bungwe la Malawi Health Equaty Network (Mhen) a George Jobe ati zomwe zachitika ku Mangochi zipereke mphunziro kwa anthu ena ofuna kupereka thandizo ku boma pa kufunika kotsata ndondomeko.
Iwo ati ofesi za boma zimasowekera thandizo losiyanasiyana ndipo ndi khumbo la boma kuti anthu akufuna kwabwino azionetsa chidwi chofuna kuchitapo kanthu.
“Chimene chidavuta apapa ndi choti Namadingo adathamanga kulemba nkhaniyi pa masamba a mchezo asanawafikire akulu akulu oyenera. Ganizo lokonza maambulansi wa ndi labwino zedi, ndipo ndilimbikitse anthu ena akufuna kwabwino kubwera poyera ndi kuthandiza pa mavuto onga awa koma adzitsata ndondomeko zoyenera” atero a Jobe.
Aka si koyamba kuti Namadingo akonze ambulansi. Ngakhale adachedwa mpaka khonsolo ya boma la Mwanza idamuopseza kuti limutengera ku khoti chifukwa kampani ya K Motors imene ankagwira nayo ntchito limodzi, Namadingo adakonza galimoto za pa chipatala cha bomalo.
Polankhula ndi wolemba nkhani wathu, woimbayu adati chilinganizo chokonza maambulansichi akuchichita payekha ndipo sakugwiranso limodzi ndi a K Motors.