Nkhani

Tipinduranji ku UNGA?

Listen to this article

Mitima ya Amalawi ili dyokodyoko kudikira zomwe mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera abweretse pochoka kumsonkhano wa atsogoleri a maiko a dziko lapansi wa United Nations General Assembly (Unga 77) omwe uli mkati ku New York m’dziko la United States of America.

Izi zili choncho poti a Chakwera ndi nthumwi 37 adanyamuka m’dziko muno kunka ku msonkhanowo kusiya mavuto a nkhaninkhani mmbuyo zomwe zachititsa ena kudzudzula ulendowo.

Ena mwa mavutowo ndi kusowa kwa mafuta a galimoto komwe kwaimitsa ntchito zambiri, kuthimathima kwa magetsi, kukwera kwa mtengo wa katundu, kusowa kwa ntchito, katangale ndi nkhawa ya pulogalamu ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya Affordable Inputs Programme (AIP).

Malingana ndi nduna yoyang’anira zaubale wa Malawi ndi maiko ena a Nancy Tembo, kumsonkhanoko, a Chakwera akakumana ndi akuluakulu ambiri komanso akakhala nawo pamisonkhano yomwe ingathetse ena mwa mavuto omwe ali mdziko muno.

“Apulezidenti akakhala nawo pamsonkhano wokambirana mfundo zachitukuko, msonkhano wokambirana zotukula maphunziro mkati mwa mliri wa Corona komanso msonkhano wokambirana zoti maiko osauka apatsidwe $18 billion yothandiza

polimbana ndi matenda a Edzi, chifuwa chachikulu ndi malungo.

“Iwo akakhala nawonso pa zokambirana zina monga zamalonda, zamalimidwe komanso akasayinira thandizo la ndalama zachitukuko ndi Millennium Challenge Corporation,” adatero a Tembo.

Nduna yoona zamaphunziro a Agness NyaLonje adati msonkhano wokhudza zamaphunziro womwe dziko la Malawi likatenge mbali udzathandiza kuyika m’chimake ndondomeko ya sukulu.

“Tidaona tonse momwe maphunziro adasokonekerera chifukwa cha mliri wa Covid-19 ndiye msonkhanowo ukaunikira kuti zoterezi zikagwa, maiko akhoza kuchita bwanji tsono mpofunika kuti Malawi ngati dziko lokhudzidwa likakhalepo,” adatero a NyaLonje.

Koma ngakhale pulogalamuyo ili choncho, mtsogoleri wakale a Peter Mutharika ati ulendowo ukusonyeza kuti a Chakwera sakukhudzidwa ndi mavuto omwe ali m’dziko muno kotero atule pansi udindo wawo ndipo kuchitike chisankho china m’masiku 90.

Koma akadaulo a zakayendetsedwe ka zinthu m’dziko ati Amalawi adikire kuti pa mndandanda wa misonkhano yomwe a Chakwera akapange, dziko la Malawi alibweretsera zotani.

A Boniface Chibwana omwe amayendetsa bungwe la zachilungamo ndi mtendere (CCJP) ati mavuto ali apo, ulendo wa a Chakwera ngofunika koma abwereko n’zakupsa kumsonkhanowo.

“Nzoonadi tili mkati mwa mavuto koma ngati apita n’cholinga chenicheni kumsonkhanowo, akhoza kukabwerako ndi mayankho a mavuto ena kumeneko ndipo izi n’zomwe Amalawi akuyembekezera,” atero a Chibwana.

Nawo a Charles Kajoloweka omwenso amatsogolera achinyamata pa zaufulu wawo m’dziko muno ati ngati boma lapita n’cholinga kumsonkhanowo, zioneka pobwerera kuti abwera n’zotani.

Iwo ati kwa zaka zambiri atsogoleri akhala akupita kumsonkhano wa Unga atagwiritsa ntchito ndalama zankhaninkhani koma osabwerako n’kanthu kooneka.

“Msonkhanowu ndi waukulu komanso wofunika chifukwa nkomwe atsogoleri amapanga maubale komanso amatolako nzeru nkupeza thandizo losiyanasiyana koma zimenezi sitidazione m’zaka zapitazi, atsogoleri amangopita n’kubwerako basi zatha,” atero a Kajoloweka.

Iwo ati a Chakwera akuyenera kuti akabwerako kumsonkhanowo, adzafotokozere Amalawi momwe ayendera ndi phindu lomwe dziko la Malawi lipeze kuchoka kuulendowo osangobwera ndi zomwe iwo anena kapena apempha.

Koma anthu onsewa kuphatikizapo a Mutharika asadalankhule zaulendowo,

kadaulo pazachuma a Milward Tobias adati n’zotheka kukhala osapita

kumsonkhanowo ngati zinthu sizili bwino m’dziko.

Iwo adati msonkhano wa Unga masiku ano udasanduka mphala yomwe atsogoleri amakangolankhula zokhudza maiko awo basi ndiye palibe chifukwa chenicheni choyendera ulendo womwe ulibe zipatso.

Kadaulo pa zamaphunziro a Limbani Nsapato ati boma likhoza kukagwiritsa ntchito msonkhanowu pokambirana ndi bungwe la International Monetary Fund (IMF) kuti lichotse mlingo wa malire a malipiro a aphunzitsi m’bajeti.

“Akuyenera kukambirana ndi IMF kuti akachotsa malirewo, alembe aphunzitsi 25 000 omwe akungokhala kuti lichepetse vuto lakusowa kwa aphunzitsi 50 000 lomwe lilipo,” atero a Nsapato.

Koma nduna ya zofalitsa nkhani yomwenso ndi mneneri wa boma, a Gospel

Kazako adati ulendo wa a Chakwera ndi wofunika kwambiri chifukwa

akakhala ndi misonkhano yambiri yapamphepete kumeneko. n

Related Articles

Back to top button
Translate »