Nkhani

Tsatsa layendaso kuchipani cha DPP

Apolisi amanga nkhwantha zitatu zachipani cha Democratic Progressive Party (DPP) powaganizira kuti anapereka malipoti abodza ku banki yokongoza maiko ndalama ya International Monetary Fund (IMF), kugulitsa banki yaboma mwachinyengo komanso katangale.

Nkhwanthazo ndi a Joseph Mwanamvekha, omwe adali nduna ya zachuma, a Dalitso Kabambe, omwe adali gavanala wa Reserve Bank of Malawi komanso a Ben Phiri, omwe adali nduna ya maboma ang’onoang’ono m’boma la DPP.

A Mwanamvekha adawamanga Lachiwiri ku Chiradzulu pomwe a Kabambe ndi Phiri adakadzipereka okha kupolisi Lachitatu atamva kuti apolisi akuwasakasaka

A Mwanamvekha ndi a Kabambe, omwe ndi ena mwa anthu 6 amene akufuna kudzaimira chipani cha DPP mu 2025, akuwazenga mlandu wopereka malipoti abodza ku IMF kuti boma la Malawi lizitengako ngongole mosavuta.

Iwowa akuti amapereka malipotiwo ndi cholinga chopereka chithunzithunzi choti chuma cha Malawi chili bwino ndipo litha kubweza ngongole mosavuta.

Malingana ndi kalata yosayinidwa ndi mneneri wapolisi a James Kadadzera, awiriwo adaphwanya lamulo potengera gawo 335 (a) la malamulo a dziko la Malawi ndipo izi zidachititsa kuti IMF isiye kuthandiza dziko la Malawi.

“Awiriwa ali m’mipando ya nduna yazachuma komanso mkulu wa banki ya Reserve adapereka malipoti abodza ku

IMF n’cholinga choti bankiyo iziwona ngati dziko la Malawi likukwaniritsa zoliyenereza kutenga ngongole koma izi zayika dziko pa moto chifukwa bankiyo idayimitsa kupeleka ngongole ku Malawi,” ikutero kalatayo.

Kalatayo yapitilira kunenena kuti a Mwanamvekha ndi nkhwantha zina za DPP zomwe sizidamangidwebe ali kale pa mpeni pa mlandu wina wogulitsa banki ya boma ya Malawi Savings Bank.

A Phiri. omwe ndi eni ake a Beata Investment adamangidwa powaganizira kuti adagula katundu mwachinyengo kudzera ku unduna woona kuti palibe kusiyana pakati pa amai ndi abambo, komanso chitukuko cha m’madera pakati pa 2018 ndi 2020.

Tsatsali likutsatira zomwe adanena mkulu wazamalamulo a Thabo Nyirenda Lolemba kuti boma likwekwesa onse omwe akukhudzidwa ndi kutumiza malipoti abodza, kugulitsa banki ya Malawi Savings ndi katangale wina aliyense.

Koma chipani cha DPP, kudzera mwa mneneri wake a Shadric Namalomba chati chikuwona kuti boma la Tonse likungofuna kuti lisokoneze aMalawi kuti ayiwale za mavuto omwe akudutsamo.

“Awona kuti akulephera kukwaniritsa zomwe adalonjeza aMalawi ndipo ayamba kale kuwafinya ndiye awona ngati njira yabwino nkuyamba kumanga anthu kuti Amalawi ayiwale mavuto,” chatero chipanicho.

Kadaulo pa ndale a George Phiri ati boma likonzekere kudzudzulidwa kuti layamba liwamba la mfiti makamaka ngati silipeza umboni wokwanira pamilandu yomwe likumangira nkhwanthazo.

Iwo ati polingalira kuti ambiri mwa omwe akumangidwawo ali pa mndandanda wa ofuna utsogoleri wa DPP, zikhoza kuonetsa ngati boma likungomangapo ngati umboni ungasowe.

Pomwe kadaulo pa zamalamulo Danwood Chirwa adati boma limangotchuka nkumanga koma silipitiriza milandu zomwe n’zolakwika.

Iwo adati pali milandu ina yomwe anthu adamangidwa chaka chatha koma pano milanduyo yayamba kuiwalika chifukwa boma langodekha osapangaponso kanthu kalikonse.

kukhala njala.AIP, chaka cha mawa

“Malipoti okhumudwitsa akutipeza koma ife tilibe polisi kapena asilikali oti angapite n’kukamanga omwe akusokoneza n’chifukwa chake tikuti boma litithandize,” atero a Njolomole.

M’madera ena akuti mavenda ndiwo akugula mmalo mwa alimi chifukwa mavendawo ndiwo akukwanitsa kupereka ndalama yoonjezera kwa ogulitsa zipangizozo.

Limodzi mwa maderawo ndi ku Ntchisi komwe apolisi amanga a mfumu a Mphamba, omwe akuwaganizira kuti amagulitsa zitupa zaunzika za anthu awo kwa mavenda kuti azikagulira zipangizozo m’maina a alimiwo.

Malingana ndi wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Ntchisi a Fatsani Mwale, amfumuwo adatenga zitupa zakutha za anthu 5 m’mudzi mwawo powauza kuti akufuna kukawapangitsira zatsopano, chonsecho akukagulitsa.

“Nkhaniyo idaphulika pa 3 December 2021 pomwe mmodzi mwa eni zitupazo adapita kumsika wa feteleza n’kukapeza chitupa chake chili ndi venda ndipo atafunsa adauzidwa kuti amfumu ndiwo amagulitsa zitupazo,” adatero a Mwale.

Bungwe lolimbana ndi ziphuphu la Anti-Corruption Bureau (ACB) nalo lati likufufuza nkhani za katangale zokhudza msika wa zipangizo zaulimi zotsika mtengo litalandira malipoti komanso litakadzionera lokha zina mwa zomwe zikuchitikazo.

“Tidayendera malo 100 ogulitsira zipangizo za AIP titalandira malipoti ndipo zina mwa zomwe zidatipezazo tidakazionadi zikuchitika moti tili ndi mafayilo ambiri omwe tatsegula kuti tifufuze,” adatero mkulu wa ACB a Martha Chizuma.

Alimi akuyenera kuombola thumba limodzi la feteleza pamtengo wa K7 500, kutanthauza kuti alimiwo akusowa K15 000 kuti aombole matumba awiri, koma malingana ndi zomwe ACB yapeza, alimi akukakamizidwa kuonjezera ndalama za pakati pa K3 000 ndi K10 000.

A Lungu avomereza kuti malipoti a mitundu yonseyi akufika kuunduna wawo koma ati undunawo ukumema alimiwo kuti azigwiritsa ntchito makomiti a m’madera mwawo pogwira anthu achinyengowo n’kukawapereka m’manja oyenera.

Makampani a Admarc ndi SFFRFM, omwe undunawo ukudalira kwambiri, agulitsako matani 27 190.7 a feteleza mmalo mwa 127 000 omwe akuyenera kugulitsa chaka chino.

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera adatsegulira pulogalamu ya AIP ya 2021 yomwe bajeti yake ndi K140.2 biliyoni pa 16 October 2021 ndipo K124.74 biliyoni ndi ya feteleza, K1.26 biliyoni ndi ya ziweto komanso K12.25 biliyoni ndi ya mbewu.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button